Kucheza
‘Phale la nkhunda sititsuka’
- Category: Kucheza
- Published Date
- Written by Bobby Kabango
Si onse omwe akaweta nkhunda zimawayanja. Ena siziswana, koma zonsezi zimachitika posatsata mwambo wa kawetedwe kake. Monga akufotokozera Pearson Kaiya wa m’mudzi mwa Safali kwa T/A Kalembo m’boma la Balaka, phale la nkhunda siliyenera kutsukidwa komanso utenge madzi komwe wagula nkhundazo. Adacheza ndi BOBBY KABANGO motere:
Wokutemera mangolomera ndi mkazi wako
- Category: Kucheza
- Published Date
- Written by Bobby Kabango
Anthu ena amakhulupirira kuti pofuna kugogoda anzawo pandewu amayenera atemere ngolomera. Ena zimawayendera pomwe ena palibe chimachitika. Malinga ndi Peason Bitoni, wa zaka 79, yemwe adatemerapo mangolomerawo, mkazi ndiye amayenera akutemere kuti zizimba zisasuluke. Kodi zimakhala bwanji? Nanga mkuluyu zinkamuthera bwanji akatemera mangolomera? BOBBY KABANGO adacheza naye.
Kukwera phiri la Mulanje sipano
- Category: Kucheza
- Published Date
- Written by Kondwani Kamiyala
Phiri la Mulanje lili ndi mbiri zambiri. KONDWANI KAMIYALA adakwera phirilo kukafika pa Chambe, ulendo wa maola anayi. Iye adacheza zina ndi zina zokhudza phirilo ndi Albert Muroma, yemwe adamuperekeza paulendowo. Adacheza motere:
Mngoni ali kuti? Onerani mthini m’mutu
- Category: Kucheza
- Published Date
- Written by Kondwani Kamiyala
Mtundu ulionse uli ndi zovala zimene zimasanthula za chikhalidwe chawo. Mwachitsanzo kunena za nyanda, maganizo a mtundu wa Achewa amabwera m’mutu. Ndipo munthu akangovala mthini, umangodziwiratu kuti Mngoni akudutsa apo. Kodi mthini n’chiyani? Kondwani Kamiyala adafuna kudziwa kuchokera kwa Isabelle Liwonde, yemwe ndi Gulupu Kanduku ya kwa T/A Kanduku m’boma la Mwanza. Adacheza motere:-
Mwambo wokumbukira mbale womwalira
- Category: Kucheza
- Published Date
- Written by Steven Pembamoyo
Anthu a mitundu yambiri amati wina akamwalira pamakhala chisoni chachikulu, kulira ndi kudandaula maka panthawi yomwe uthenga wa malilowo wafikira komanso panthawi yoika wakufayo m’manda. Mwambo wonse ukatha olira aja amaiwala ndi kumapanga zina koma pakapita nthawi otsala aja amakonza tsiku lomwe amakawaka mtumbira ya wakufayo pamwambo wa chiliza. Ena amaona ngati kumanga chilizacho n’kunyada chabe koma Agnes Kampakeni akuti chiliza chili ndi tanthauzo lake ndipo STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere:
Kupeperera mtera kumatheka ndi chuni
- Category: Kucheza
- Published Date
- Written by Steven Pembamoyo
Pokonza mankhwala pamakhala miyambo yosiyanasiyana. Chuni ndi dzina la chipinda chokhudzana ndi mankhwala a zitsamba. Steven Pembamoyo adacheza ndi sing’anga akufotokoza za chuni motere:
Kuteteza makanda ndi mphini
- Category: Kucheza
- Published Date
- Written by Solomon Manda
Zikhulupiriro zina zamakolo zimalimbikitsa kuti khanda lizitemedwa mphini litangobadwa. Kodi zimenezi zinali ndi phindu lanji? Nanga masiku ano khalidweli likukhala ngati likuchepa chifukwa chiyani?SOLOMON MANDA adacheza motere pankhaniyi ndi gogo Tereza Jiya wa m’mudzi mwa Buleya kwa T/A Kapeni m’boma la Blantyre:
Mbiri ya Mtayanyemba ku Neno
- Category: Kucheza
- Published Date
- Written by Bobby Kabango
Maina a madera ena koma ali ndi nkhani. Ku Neno kuli malo ena otchedwa Mtayanyemba. Dzinali kuti liperekedwe akuti padali nkhani. Ambiri akalowera kumeneko akuti amasaka chiyambi cha malowo. BOBBY KABANGO adali kumeneko ndipo adacheza ndi Nyakwawa Benito pa nkhani ya dzinali.
Chisamba: Gule wovinira anamwali
- Category: Kucheza
- Published Date
- Written by Steven Pembamoyo
Magule ena ndi ongokometsera zochitika, koma pali ena omwe ali ndi tanthauzo lake. Apa tikusanthula za gule wa chisamba yemwe amavinidwa pakati pa Achewa. STEVEN PEMBAMOYO akucheza ndi Alinesi Kamchisa wochokera kwa T/A Kalolo ku Lilongwe yemwe akufotokoza za guleyu motere:
Kasenye: Nyama yopininga woipha
- Category: Kucheza
- Published Date
- Written by Bobby Kabango
Ukapha nyama zina konzekera mavuto kwa iwe komanso kwa chida chomwe unagwiritsira ntchito. Nyama yomwe imasokoneza alenje ndi kasenye. Kanyamaka kamakhala ngati gwape koma iko akuti kamapininga ukakapha. Kodi izi zimachitika chifukwa chiyani? BOBBY KABANGO akucheza ndi Saopa Mukitiha wa m’mudzi mwa Nacheya kwa T/A Chiwalo m’boma la Phalombe yemwe wachita uzimba kwa zaka.
