Nation Online

Monday, May 20th

You are here: Home Tamvani Kucheza Mbiri ya Chiendausiku ku Balaka

Mbiri ya Chiendausiku ku Balaka

Maina ambiri kuti aperekedwe pamakhala nkhani yaikulu. Ena amabwera chifukwa cha milandu. Dzina la Chiendausiku ndi dzina la dera lomwe likupezeka pa mtunda wa makilomita 8 kuchokera padepoti ya Balaka kutenga msewu wa Zomba. Derali lili ndi nkhani yaikulu kuti lifike povala dzinali. BOBBY KABANGO adacheza ndi Alason Kamazizwa wa kumeneko momwe dzinali lidabwerera.

Tidziwanetu….

Ndine mlimi wochokera m’mudzi mwa Chikololere kwa Gulupu Chiendausiku kwa T/A Nsamala m’boma la Balaka. Kupatula izo, ndikutsogolera gulu lobwezeretsa chikhalidwe cha Angoni kwathuko ndipo timakumana ndi Angoni anzathu ku Lizulu. Ndili ndi zaka 71.

Takambani za chiyambi cha dzina la Chiendausiku?

Nkovuta kunena kuti dzinali lidabwera chonchi chifukwa idali nkhani yaikulu. Bwanji mundilole nditambasule nkhaniyi kuti mumvetse komanso dziwani kuti ngakhale dzina la mudzi womwe ndikukhalawu uli ndi nkhani yake.

Masukani Angoni....

Kale mudziwa kuti Angoni amakhala ku South Africa ndiye atayamba kumenyana kumeneko adayenda mokwera ndikutulukira ku Mozambique kuchoka uko adafika pa Lizulu ndikupeza malo omwe amakhala. Mmenemotu ndi mma 1800.

Amatsogozedwa ndi ndani ku Lizuluko?

Chikuse ndiye amawatsogolera monga mfumu yawo. Chikuseyo ndiye Gomani woyamba yemwe ufumu wake wasefukira mpaka lero. Tsono atafika kumeneko amalimbanabe ndi anthu amitundu yosiyanasiyana kuti ayigonjetse pofuna kuti atenge malo. Padali Alhomwe, Ayawo ndi Achewa omwe amalimbana nawo kuti atenge malowo.

Amalimbana nawo kuti atani? Nanga amalimbirana kuti?

Cholinga cha Angoni kudali kulanda malo kuti akhale awo. Izi zimachitika ku Balaka kuno, Mangochi ndi madera ena ozungulira. Koma panthawiyo adapeza kuti ku Liwonde kukufuna kulowa adani. Apo Chikuse adauza Chiendausiku ndi Chikololere kuti akathane nawo kuti asawoloke mtsinje wa Shire.

Kusonyeza kuti mainawa n’kuti ataperekedwa kale? Tatambasulani bwino….

Mwanena zoona. Tsono chomwe chidachitika n’kuti panthawi yomwe Angoniwa amakhala ku Lizulu, padali adani ena omwe amayambana nawo. Apo ndipomwe Chikuse adasankha gulu loti liziyenda ndi usiku cholinga choti azithana ndi adani pomwe iwo akugona. Masana pomwe anthu ali kokamenya nkhondo gulu loyenda ndi usikuli silimakhala nawo koma usiku amakhala ali komenya nkhondo pomwe adani akugona. Amenewa amangotchedwa achiendausiku. Yemwe amatsogolera gululo adapatsidwa dzina la Chiendausiku monga mwa ntchito yake.

Mwati uku kudali ku Lizulu, zidakhala bwanji kuti lipezeke ku Balaka?

Tsono chomwe chidachitika nchakuti ku Liwonde kumafuna kulowa adani monga ndafotokoza kale. Chikuse adatuma Chiendausiku kuti akathane ndi adaniwo komwe adalinso ndi Chikololere. Nkhondo itatha aliyense adali ndi mwayi wosankha malo omwe afuna akakhale chifukwa adani adali atathawa. Iwo adakasankha kukakhala kumeneku komwe pano kukutchedwa Chiendausiku.

Ndimayesatu Chiendausiku ndi dera chabe?

Pambali potchuka ngati dera, gulupu ameneyu ali ndi nyakwawa zoposa khumi. Ambiri amaganiza kuti ndi malo. Komanso dziwani kuti ufumuwo adawuvala woyambirira ndi a Chiendausiku omwe adamenya nkhondo mpaka pano ulipo mopitirizidwa ndi ana.

Nanga la Chikololere lidadza bwanji?

Mudzi wa Chikololere amakolola chimanga chambiri zaka zonse ndiye mfumu yawo imangotchedwa Chikololere. Mpaka lero dzinali silichoka.

Alipo omwe akuyendabe usiku pano? Nanga zokololazo zikukololeredwabe?

Ayi awa tsopano ndi maina chabe. Malinga ndi kusintha kwa nyengo kukolola kukukhala kovuta bola nthawi imeneyo zimayenda.

Add comment

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.


Security code
Refresh