Nation Online

Wednesday, May 22nd

You are here: Home Tamvani Kucheza Vimbuza: Nthenda yolira gule

Vimbuza: Nthenda yolira gule

Masiku ano, pamisonkhano yosiyanasiyana, pamapezeka magulenso osiyanasiyana. Gule wochititsa chidwi wina amene amagundika ndi wa vimbuza. Koma momwe akufotokozera Mfumu Kayiwale ya m’boma la Rumphi, kuvina vimbuza pamsonkhano ndi manyado chabe. Vimbuza ndi matenda, ndipo kuti munthu achire, pamakhala mwambo. Akucheza ndi EDWIN NYIRONGO motere:

Kodi vimbuza ndi chiyani?

Vimbuza ndi matenda. Anthu amadwala ndithu ndipo zikatere amafuna mankhwala choncho anthu amachira. Koma kuti munthu achire, amamuombera m’manja ndikuliza ng’oma iyeyo nkumavina kuti matenda aja achoke. Pali vimbuza zosiyana. Munthu akagwidwa ndi vanusi, zimadzuka choncho munthu uja amavina. Chimbuza chimaitanitsa kamwana ka nkhuku. Komanso ngati chinali chimbuza cha chanusi, wodwalayo amafuna mankhwala oti anzache achire.

Tafotokozani bwino lomwe mitundu ya vimbuza...

Pali chanusi, mphanda ndi chimbuza chabe. Chikakhala chanusi, ndi chija chimapanga phokoso kuti yi-yi-yi-yi. Chimakuuzanso mtengo woti ukakumbe pa matenda omwe iwe kapena mbale wako wadwala. Chimbuza chachabe ndi chija umamva mutu kapena m’thupi kupweteka ndiye umavina kuti uchire, ukhale bwino.

Makamaka vimbuza zimayamba nthawi yanji?

Nthawi zambiri imakhala nthawi yadzuwa, nthawi ija yoti mvula ikufuna kubwera choncho fumbi lija ndi kafungo kaja kamabwera ndi mvula kamadzindula mtima.

Mukunena kuti vimbuza ndimatenda oti kuchipatala siungachire?

Ngakhale mpang’ono pomwe siungachire. Panali anthu amene amadziwa mankhwala ache. Ndichifukwa chache ena amapita kuchipatala nthawi zambiri koma osachira.

Chifukwa nchiyani nthawi zambiri amagwidwa vimbuza ndi amayi?

Zimakhaladi choncho kuti ambiri amene amakhala ndi vimbuza ndi amayi. Koma tisaiwale kuti chinthu chikachitika, amayi ndi amene amagwidwa msanga. Komanso mwamuna akagwidwa ndi vimbuza kumakhala kovuta kuti akavine pagulu. Ena amuna amene akuvina masiku ano ndi manyado chabe koma amuna amatenda pamakhala povutirapo kukavina.

Ndiye pali kubunyesera; pamene munthu amamuvindikira ndi nsalu nkhope ataiyang’anitsa pamphika pomwe pali utsi wa mankhwala. Sikukakamiza vimbuza?

Iyayi. Kumakhala kusaka matenda. Ngakhale munthu ukapita kuchipatala, adotolo amasaka chimene ukudwala, chija pachizungu amati examination. Kumakhala kuona ngati uli ndi vimbuza. Mumphika muja amaikamo mankhwala ndicholinga choti ngati ndi vimbuza, vituluka koma ngati sivimbuza sivituluka. Koma nthawi yonseyi ng’oma zimakhala zukulira.

Tsopano munthu wa vimbuza akavina amachira. Koma pakadutsa kanthawi amaitanitsa ng’oma kuti avinenso. Vimbuza vimakhala kuti vabweranso?

Zili pawiri; ngati vimbuza mwavizoloweretsa kuvina, ndiye uzivinabe, koma ena amavina kenako kumwa mankhwala basi osadzavinanso. Ena aja amapitiriza kuvina amakhala kuti sanamwe mankhwala wotseka. Koma ena amangovinira manyado chabe.

Pamenepo mubwerezepo; masiku ano muzikondwerelo zosiyanasiyana anthu akumavina vimbuza. Ndimatendanso nanga?

Malingana ndi mwambo wa Chitumbuka, vimbuza ndi matenda. Koma masiku ano pakumakhala misonkhano kaya wachipani kaya wa magulu osiyanasiyana, vimbuza vimakavinidwa. Pamene paja vimbuza vimatengedwa ngati voseweretsa. Mwina ndinenenso motere: vimbuza ndi matenda komanso vimakhala ngati mwambo wa Chitumbuka. Mwina poopa kuti mwambo umenewu ungathe, anthu akumazitenga zoseweretsa nkuyamba kuvina pagulu. Koma ambiri amene amavina anali ndi vimbuza kale.

Mwati n’chifukwa chiyani vimbuza vimayamba nthawi yoti mvula yatsala pang’ono kubwera?

Zimadana ndi fungo ladothi nthawi yoti mvula ikubwera. Komanso mvula ikagwa pamakhala masamba omwe timati a nyungu (a mawungu) yosakhwima amene munthu akadya, amabweretsa matenda ngati vimbuza. Zimakhala ngati munthu amene wadya nyama yomwe imamuwenga. Chonchonso masamba a mawungu kwa anthu ena.

Chifukwa chiyani nthawi zambiri vimbuza vimakhalako usiku?

Chimene chimachitika ndichakuti munthu akavina, amangomanga kena kache mumabere koma msana wonse umakhala panja. Ndiye ambiri amachita manyazi nthawi ya masana choncho anaganiza kuti vimbuza vizikhalako usiku. Komanso ena mwa anthu odwala vimbuza ena amakhala akamwani. Umakhala ulemu wapadera kuti anthu ngati amenewa azivina usiku chifukwa saona anthu kwambiri.

Ku Rumphi kuno kunali munthu wotchuka ndi vimbuza amati Siyayo Mkandawire, mumamudziwa?

Ndimangomumva chabe.

Ndiye nawonso anali matenda?

Zimayamba ngati matenda. Koma mmene ndanenera muja kuti pamakhala anthu amene amatseka kuti vimbuza vija visabwerenso. Ena mwa anthu amenewa amakhala woti akufunabe kuvina. Ndi anthu ambiri mukuwawonawa akuvina mu zisangalalo.

Kodi amene amagwidwa ndi vimbuza ndi Atumbuka okha kapenanso mitundu inanso?

Mitundu ina itha kugwidwa ndi vimbuza. Koma makamaka ndi Atumbuka ndi Abiza aku Zambia. Musaiwale kuti masiku ano mitundu yalowelerana. Ndichifukwa chakee mumva kuti ku Nkhata Bay kuli vimbuza, kapena ukunso kuli vimbuza. Ndichifukwa choti talowelerana koma matendawa ndi a Atumbuka.

Komanso pali zovala. Ena amavala zosokosa mu miyendo kapena mchiuno. Ndizachiyani zimenezi?

Zovala zimakhala mangenjeza, mazamba ndi nyisi. Zimakhala zokometsera. Mangenjeza akamalira, amagwirizana ndi ng’oma.

Ndiye mwati mankhwala a vimbuza alipo ndithu?

Mankhwala alipo, koma masiku ano walowa ndi utambwali kapena tinene kuti ukhuluku. Kale, munthu sungakhale sing’anga usanadwale. Koma masiku ano asing’anga achuluka, ndi ena oti sanadwalepo. Panalidi asing’anga ena oti sanadwalepo koma amakhala oti makolo awo anali asing’anga ndiye iwowo aphunzitsidwa. Amenewa anali asing’anga enieni, osati zamasiku anozi zofuna kudyera anthu makobiri.

Koma makhwala ake ndikuvina basi?

Kuvina, komanso amakupatsa mbuzi kapena nkhuku kuti umwe magazi ake mochita kukoka, amati kusawiska. Akasawiska, basi nthawi zina utha kumavina nthawi zina ayi.

Amasankha ndani kuti umwe magazi a mbuzi kapena nkhuku?

Ndi matenda amene amakuuza. Mtundu wa matenda omwe uli nawo ndi umene umakuuza nkuti ndikufuna magazi a nyama ya nkhuku, kapena mbuzi kapena kungomwa dzira losaphika.

 

 

Add comment

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.


Security code
Refresh