Nation Online

Wednesday, May 22nd

You are here: Home Tamvani Kucheza Cwala: Mwambo wodalitsa zokolola

Cwala: Mwambo wodalitsa zokolola

Sabata yatha Angoni m’dziko muno anali ndi mwambo wa Cwala ku Zambia pamodzi ndi Angoni ena ochokera m’maiko ena muno mu Africa. Mwambowu umachitika chaka ndi chaka. STEVEN PEMBAMOYO akufufuza zambiri za mwambowu kuchokela kwa wa pampando wa gulu la angoni a kwa Mlonyeni ku Mchinji Niron Phiri yemwe akufotokoza motere:

Mukuoneka okonzeka komanso a paulendo kodi ulendo umenewu n’ngwakuti?

Ulendo umenewu ndiwopita ku Mtengule ku Zambia kwa mfumu yaikulu ya Angoni Inkosi Mpezeni komwe kuli mwambo waukulu kwambiri wa Chingoni umene umatchedwa Cwala.

Cwala ndi mwambo wanji?

Cwala ndi mwambo osangalala, kuthokoza Mulungu komanso kudalitsa mbewu zomwe zikucha kumene.

Mwambowu umachitika nthawi yanji?

Mwambo umenewu umachitika sabata ziwiri zomalizira za mwezi wa February pomwe mbewu zambiri m’minda zimakhala zitacha ndiye timafuna kuti anthu asanayambe kudya kapena kugulitsa tizidalitse kaye komanso tiyamike Mulungu potipatsa zokololazo.

Kumwambo wa Cwala kumakhala zotani?

Kumwambowu kumachitika zambiri koma chachikulu ndichakuti kumakhala mpikisano ovina ingoma ochokera m’maiko osiyanasiyana komanso kumakhala kukambirana nkhani zosiyanasiyana zokhudza chikhalidwe chathu.

Mwambowu udayamba liti?

Mwambowu udayamba m’zaka za m’ma 1980 ku South Africa ndipo adayambitsa ndi Inkosi Mpezeni 4. Umakhaladi mwambo waukulu chifukwa Angoni osiyanasiyana amakumana malo amodzi kunyadira chikhalidwe chawo.

Kupatula kubweretsa Angoni pamodzi komanso kudalitsa zakumunda kufunika kwina kwa mwambowu ndikotani?

Kufunika kwina ndikwakuti mwambowu umatithandiza kusunga chikhalidwe cha Angoni chifukwa ana athu amakhala akuphunzira zomwe zimafunika pa chingoni komanso ndinthawi yomwe ana amatha kulandira malango kuchoka kwa akuluakulu.

Mwanenapo za ana kodi tinene kuti ana nawonso amaloledwa kupita ku mwambowu?

Palibe choletsa ngakhalenso amayi nanga siamene amakometsera Ingoma ndi thungululu. Chomwe chingakanikitse munthu kupita nawo ndi ndalama zoyendera komanso zogulira chakudya kumeneko.

Tinene kuti aliyense amapita payekhapayekha ndi banja lake kapena zimakhala bwanji?

Ayi. Timasonkherana ndalama yopezera galimoto yoti idzatitenge komanso ndalama zina zogulira chakudya. Ndiye tikafika kumeneko amatipatsa malo amodzi okhalapo kawirikawiri amatikhazika pa sukulu ya Chankhanga yomwe ili pafupi ndi malo omwe mwambowo umachitikira.

Mwambowo mumauyendetsa motani?

Pamakhala ndithu munthu otsogolera monga zikhalira pamwambo ulionse. Iyeyu amalengeza chomwe chichitike chikatha chomwe chikuchitika panopa ndiye anthu komanso magulu amakhala okonzekeratu kudikira nthawi yawo.

Kodi omwe si Angoni koma akufuna kupita nawo amaloledwa?

Zimatengera chifukwa chopitiracho chifukwa ndanena kale paja kuti ndi mwambo wa Angoni kutanthauza kuti Angoni okhaokha ndiamene amaloledwa kutengapo mbali koma anthu a mitundu ina amene akufuna kungowonerera amaloledwa kutero.

Umakhala mwambo wamasiku angati?

Umatenga masiku atatu basi kuchokera tsiku lotsegulira kenako takabwerera m’makwathu anthu amayamba kudya za m’minda mwawo.

M’malawi muno muli Angoni ochokera m’maboma osiyanasiyana tinene kuti nonse mumanyamukira pamodzi?

Ayi koma tikafika kumeneko timakhala limodzi ngati Amalawi ndikumachitira zinthu pamodzi.

 

Add comment

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.


Security code
Refresh