Masewero
Apolisi apulumutsa chimango kayira
- Category: Masewero
- Published Date
- Written by Garry Chirwa
Apolisi Lachiwiri lapitali adapulumutsa Chimango ‘Blackberry’ Kayira pamene ena mwa onenerera timu ya Big Bullets ankafuna kumpanda pa Kamuzu Stadium.
Chilemba, bellew abwerezananso
- Category: Masewero
- Published Date
- Written by Peter Kanjere
Katswiri wa nkhonya Isaac ‘Golden Boy’ Chilemba wati akufunitsitsa kumenyananso ndi Anthony Bellew awiriwa atalepherana Loweruka ku Liverpool pankhonya yofuna kupeza yemwe adzaswane ndi Chad Dawson wa ku Mangalande.
Chilemba, yemwe adabadwira ndi kukulira ku Blantyre koma pano amakhala ku South Africa, adakwiya kuti majaji atatu adagamula kuti padalibe wopambana pa nkhonyayi.
Mwawi agwedeza ligi ku australia
- Category: Masewero
- Published Date
- Written by Singayazi Kaminjolo
Mbiri ya katswiri wosewera mpira wa manja Mwawi Kumwenda ikupitabe patsogolo mudziko la Australia kaamba kaluso lake muligi ya Victorian Netball League (VNL).
Kim adzipereka kuitana Flames m’dziko la Denmark
- Category: Masewero
- Published Date
- Written by Staff Writer
Mphunzitsi wakale wa timu ya dziko lino Kim Splidsboel wati Flames ikhoza kukakonzekera masewero ake ndi timu ya Nigeria m’dziko lake la Denmark.
Izi zidadziwika timuyo itagonjetsa timu ya dziko la Namibia pamasewero ofuna kupeza matimu amene adzakasewere nawo mumpikisano wa World Cup ku Brazil.
Ligi iyamba lero
- Category: Masewero
- Published Date
- Written by Peter Kanjere
Mpikisano wa TNM Super League wa chaka cha 2013/2014 uyamba lero m’zigawo zonse zitatu pamene mipira isanu ndi inayi iseweredwe.
Flames ipumunthana ndi namibia lero
- Category: Masewero
- Published Date
- Written by Garry Chirwa
Timu ya mpira ya dziko lino ya Flames yati ndi zotheka kuthambitsa timu ya Namibia lero mumpikisano wa 2014 World Cup.
Carlsberg ithandiza BB, Manoma
- Category: Masewero
- Published Date
- Written by Singayazi Kaminjolo
Kampani yofulula mowa wa Carlsberg ya Bottling and Brewing Group Limited (BBGL) yakhumudwitsa masapota a matimu a Big Bullets ndi Wanderers chifukwa chokanika kukwaniritsa lonjeza lake.
Nkhani ya nyumba za Flames ivuta
- Category: Masewero
- Published Date
- Written by Peter Kanjere
Pali kukaikitsa pa zolinga za nduna ya zamasewero Enock Chihana kuti anyamata osewera mutimu ya mpira ya dziko lino ya Flames apeze mpata wokhala munyumba za Malawi Housing Corporation.
Chisankho cha NAM lero
- Category: Masewero
- Published Date
- Written by Garry Chirwa
Zonse zokonzekera chisankho cha bungwe loyendetsa mpira wa ntchemberembaye m’dziko muno la Netball Association of Malawi (NAM) chimene chichitike lero mumzinda wa Mzuzu zatha.
Ndipo nkhani yomwe ili mkamwamkamwa ndi mpikisano wolimbirana udindo wa pulezidenti pakati pa Rosy Chinunda yemwe apikisane ndi Khungekile Matiya.
Kubwerera kwa fischer kwautsa mapiri pachigwa
- Category: Masewero
- Published Date
- Written by Singayazi Kaminjolo
Zomwe wachita mphuzutsi watsopano wa timu yampira wamiyendo ya dziko lino ya Flames, Edington Ng’onamo posankha Fischer Kondowe kuti akhale nawo mukampu ya anyamata omwe akukonzekera kudzamenya ndi timu ya Namibia mu Wolrd Cup zadabwitsa anthu ena omwe akuti Kondowe siwoyenera kumenya mu Flames.
