Nation Online

Wednesday, May 22nd

You are here: Home Tamvani Masewero Ng’onamo wati ndiwokonzeka

Ng’onamo wati ndiwokonzeka

Mphunzitsi wa timu ya Big Bullets Eddington Ng’onamo yemwe wasankhidwa kulowa m’malo mwa Kinnah Phiri ngati mphunzitsi wa timu ya mpira ya dziko lino mongogwirizira, wati ndiwokonzeka kugwira ntchitoyi.

Bungwe loyang’anira masewero a mpira m’dziko muno la FAM posachedwapa lidasankha Ng’onamo kukhala mphunzitsi wa timu ya Flames ndipo akatswiri akale a timuyi Ernest Mtawali ndi Patrick Mabedi ndiwo adasankhidwa kuti akhale omuthandizira ake.

Bungwe la FAM lidasankhanso Charles Manda kukhala timu maninjala komanso kaputeni Kondwani Kachipanda ngati dotolo.

Pofotokozera mtolankhani wa Tamvani sabata ino, Ng’onamo adati ndiwokonzeka kuyamba kugwira ntchitoyi nthawi iliyonse.

“Ndikungoyembekezera kuti a FAM amalizitse ndondomeko ndi aku boma koma ndine wokonzeka ndithu kuthandiza dziko langa kudzera mu timu ya Flames,” adatero Ng’onamo.

Iye anatinso ndi wokondwa kuti FAM yasankha Mtawali ndi Mabedi kukhala omuthandizira ake.

“Mtawali ndi Mabedi ndikuwadziwa bwino. Ndi anthu amene ali ndi luso la mpira atasewera kwa nyengo yayitali ndipo ndiri ndi chikhulupiliro kuti ndigwira nawo bwino ntchito,” anatero Ng’onamo.

Nawonso Mtawali ndi Mabedi anati ndiwokonzeka kuthandiza Ng’onamo.

“Tikungoyembekezera kuti a FAm atifotokozere kuti nkhani ya malipiro ikhala bwanji, koma ndife okonzeka kuthandiza dziko lathu,” anatero Mtawali

Pulezidenti wa bungwe la FAM Walter Nyamilandu wati asanuwa ayamba ntchito yawo zokambirana ndi boma kulingana ndi nkhani za malipiro awo.

“Tiri ndi chikhulupiliro kuti ikamatha sabata ino, boma likhala litabvomereza zomwe tidapempha kulingana ndi malipiro a makochiwa.

“Zonse zikayenda bwino, onsewa akuyenera kuyamba ntchito yawo kumayambiriro a mwezi wamawawu,” anatero Nyamilandu.

Timu ya Flames idzasewera ndi timu ya Namibia mu mpikisano wa dziko lonse wa World Cup pa 22 March mu mzinda wa Windhoek ku Namibia.

Awa adzakhala masewero oyamba a Ng’onamo komanso omuthandizira ake.

Add comment

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.


Security code
Refresh