Ana opempha m’matawuni
- Category: Masewero
- Written by Rabecca Theu
Ndidali mmodzi wa omwe amakhudzidwa ndi ana opempha mimsewu ya m’matauni ndi mizinda yosiyasiyana kufikira masiku apitawa pomwe maganizo anga adasintha.
Adayamba kundisokoneza adali mwana wina yemwe atandipempha sindidampatse chifukwa ndinalibe chomupatsa, koma kutukwana adanditukwana apo kudali kodabwitsa.
Kenaka madzulo ena ndili m’tauni ya Blantyre masiku apitawa, kamnyamata kooneka ka zaka zitatu kadandiyandikira nkundidandaulira kuti ndikathandize kali ndi njala.
Dandaulo la njala lili apo, malingaliro anga adali poti mwana wachichepereyu amatani yekhayekha m’tauni nthawi yotaikayi, mvula ikugwa.
Pomufunsa adati ali yekha koma atapanikizidwa ndipomwe adaloza mayi ake omwe adali ataima pakhonde yasitilo pakatali ndithu.
Adali mayi wabwinobwino ndithu, atabereka mwana wina kumsana kachikwama ka katundu kali pambalipa.
Chachidziwikire cholinga cha mayiyu chinali chakuti mwanayo ndiye anzinka napempha podziwa kuti anthu angakhudzike ndi kuvutika kwa mwana kuposa umo mayiyo angamvetsere chisoni.
Achuluka amayi ndi abambo ngati awa m’taunimu omwe amachita chilichonse chotheka posaka ndalama popempha.
Pambali ponena bodza kwa anthu omwe akupemphako, amagwiritsa ntchito ana ngati nyambo yopezera kangachepe.
Amanyamula katundu ngati ali paulendo omwe wadulidwa panjira ndi zovuta zina kuti opemphedwawe umve chisoni.
Kodi uku sikuba komwe?
Nkutheka alipo ena omwe amapempha pachione koma zochitika ngati izi zikundichititsa kulingalira ngati nkoyenera kuthandiza anthu ngati awa.
