Nation Online

Tuesday, May 21st

You are here: Home Tamvani Masewero Super League itha mawa

Super League itha mawa

Mpikisano wa TNM Super League ufika kumalecheleche mawa pamene matimu amalize mipira yawo ndipo Silver Strikers ikuoneka kuti itenganso chikho kachitatu motsatizana.

Silver ikuoneka kuti yatenga kale chikhochi popeza ili ndi mapointsi 58  pamene Bullets ili ndi 55. Matimu awiriwa atsala ndi mpira umodzi umodzi.

Silver imaliza ndime yake pokumana ndi Mighty Wanderers pa Civo Stadium mawa pamene Bullets ikunthane ndi Red Lions ku Kamuzu Stadium.

Zinthu zikukomera Silver chifukwa idachinya zigoli zambiri ndiye ngakhale atagonja mawa ku Wanderers n’zovuta kuti Bullets, ngati ichinye Lions ndikufikanso pa mapointsi 58, kuti ipitirire Silver.

Malinga ndi kuonkhetsa, Bullets iyenera kupambana ndi zigoli khumi kuti itenge chikhochi itafika pa mapointsi 58.

Koma ngakhale Bullets ifike pa mapointsi 58, zitengera kuti Silver isalepherane kapena kuchinya Wanderers popeza Silver ikangotero ulendo wa Bullets wofuna chikho uthera pomwepo.

Ngakhale itagonja kwa Wanderers, Silver ikhoza kutengabe chikho ngati Bullets sikwanitsa kuchinya Lions ndi zigoli zoposa khumi kwa duu.

Mlembi wa Silver Owen Munthali adanenetsa kuti iwo asewera moikapo mtima komanso mosaderera Wanderers mawa.

“Kuti tifike pano tadutsa m’zokhoma zambiri ndiye tiyesetsa kuchinya Wanderers ndi kutenga chikhochi. Tikufunitsitsa kumaliza ligi ndi kupambana chifukwa akuluakulu athu abwera kudzawonera masewelowo,” Munthali adatero.

Pamipira ina, Azam Tigers adakumana dzulo ndi Blantyre United yomwe lero iswanenso ndi Epac FC ku Kamuzu Stadium lero. United ikufuna kumaliza yachitatu popeza idali ndi 48 points pamene timalemba nkhaniyi.

Ku Chitowe Stadium ku Dwangwa, Mighty Wanderers isewera ndi Mafco kenako, Manoma apita ku Civo Stadium mawa kukakwangula ndi Silver.

Pansi paligiyi pali, Kabwafu United, Escom United ndi Bvumbwe Research omwe atuluka mu Super League ndikubwelela ku mipikisano ya chigawo cha kumpoto ndi kumwera. Wopambana muzigawozi adzalowa mu Super League, malingana ndi malamulo a Super League of Malawi.

Pa zigoli, Vincent Chinthenga wa Bvumbwe atenga mphoto yaukatswiri wochinya ndi zigoli 18.

Add comment

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.


Security code
Refresh