Nation Online

Sunday, May 19th

You are here: Home Tamvani Masewero Kubwerera kwa fischer kwautsa mapiri pachigwa

Kubwerera kwa fischer kwautsa mapiri pachigwa

Zomwe wachita mphuzutsi watsopano wa timu yampira wamiyendo ya dziko lino ya Flames, Edington Ng’onamo posankha Fischer Kondowe kuti akhale nawo mukampu ya anyamata omwe akukonzekera kudzamenya ndi timu ya Namibia mu Wolrd Cup zadabwitsa anthu ena omwe akuti Kondowe siwoyenera kumenya mu Flames.

Kondowe wakhala nthawi yaitali asakusewera mu Flames chifukwa chosepmphana ndi mphunzitsi wakale Kinnah Phiri kaamba ka khalidwe lake.

“Apa Ng’onamo sadaganize bwino. Kondowe anatha ndipo luso lake silili mwakale. Pali anyamata ambiri m’dziko muno omwe akumenya mpira wabwino kuposa Kondowe,” adatero mkulu wina yemwe ali mukomiti yaikulu yoyendetsa mpira wa miyendo m’dziko muno koma sadafune kutchulidwa.

“Sikuti tikudana ndi Bullets, koma kunena chilungamo Kondowe amasewera mpira wotani woti mpaka kuitanidwa kukampu. Ng’onamo apa akuonetsa kukondera timu yake ya Bullets,” adatero mkuluyi.

Lapken Mmangisa yemwe ndi wotsatira timu ya Flames naye sakugwirizana ndi Ng’onamo.

“Izi si zoona ndipo ndi zodabwitsa. Zikuonetsa kuti a Ng’onamo angomuyitanitsa Fischer chifukwa amachoka mu Big Bullets. Nanga tingati amutenga chifukwa cha luso? Luso lake liti? Fischer anali kale pano wakula sangathamange monga mwakale,” adatero Mmangisa.

Koma Ng’onamo, otsatira ake Ernest Mtawali komanso Patrick Mabedi ati Kondowe wakhala akumenya bwino kwambiri ku Bullets ndipo ndi koyenera kuti amupatse mwayi mu Flames.

“Ngati pali munthu mmodzi yemwe akuchita bwino ku training ndiye ndi Fischer. Kuweruza munthu molakwika kumapha mpira. Kondowe wakhala akuchita bwino kwambiri mu Bullets ndipo wakhala akutenga u-man of the match kangapo. Izi zikusonyeza kuti ali bwino. Ife tamupatsa mwayi kuti awonetse ngati kuti akhoza kumenya mu Flames,” adatero Mtawali.

Mabedi naye wati Kondowe ndi mkhalakale pa mpira ndipo ndiwolimbikira kwambiri.

“Fischer wamenya mpira m’maligi apamwamba. Ndili ndi chikhulupiriro kuti atithandiza,” adatero Mabedi

Comments  

 
0 #1 owen 2013-03-11 17:11
Fischer is old now we nid fresh legs!!
Quote
 

Add comment

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.


Security code
Refresh