Chichewa

TCC imema alimi a fodya kulembetsa

 

Bungwe loyang’anira za malonda a fodya m’dziko muno la Tobacco Control Commission (TCC) lati alimi a fodya omwe sadalembetse nkulipira zitupa zawo alembetseretu kuti akhale nawo mkaundula wa alimi a fodya.

Chikalata chomwe bungweli latulutsa chati pofika mwezi wa June chaka chatha, alimi 29 861 ndiwo adali atalembetsa nkulipira zitupa zawo.

 Alimi ayenera kulembetsa m’kaundula nthawi isanathe
Alimi ayenera kulembetsa m’kaundula nthawi isanathe

Kutsika kwa chiwerengerochi kwapangitsa kuti bungwe la TCC liwonjezere nthawi yomwe alimi angakalembetsere ndi kulipira zitupa zawo zogulitsira fodya chaka chino mpaka pa 29 January 2016.

“Malingana ndi chiwerengero cha alimi omwe alembetsa ndi kulipira ziphaso zawo, taganiza zoonjezera nthawi yolembetsera ndi kulipira kuti alimi omwe sadatero akhale ndi mpata. Alimi onse omwe sadalembetse kapena kulipira ziphaso zawo apangiretu nyengo yoonjezerayi,” chatero chikalatacho.

Mkulu woyang’anira za ubale wa wa bungweli ndi makampani kapena nthambi zina Mark Ndipita adati vutoli ladza kaamba ka zovuta zingapo monga zokhudza malonda a fodya.

“Tikuganiza kuti mwina alimi ena akadali otangwanidwa ndi nkhani zokhudza malonda a chaka chatha komanso zochitika zina zosiyanasiyana monga mudziwa mmene nkhani ya fodya imakhalira,” adatero Ndipita.

Iye adati ngakhale zinthu zili choncho, si kuti malonda a fodya a chaka chino asokonekera poti alimi a fodya amayendera mlingo wa fodya omwe amapereka a TCC ndipo umaonetsedwa pa chitupa.

Mkulu wa TCC Albert Changaya, adauza nyuzipepala ya The Nation kuti ogula fodya akunja atsitsa mlingo wa fodya yemwe agule chaka chino kuchoka pa makilogalamu 192.6 miliyoni chaka chatha kufika pa 177 miliyoni.

Changaya sadafotokoze chomwe chapangitsa kuti mlingowu utsike komanso ngati izi zikutanthauza kuti atsitsa mlingo a fodya pa zitupa za alimi pokakhomera.

Fodya ndi mbewu yomwe dziko la Malawi limadalira kwambiri pachuma chake koma pakatipa malonda a fodya akhala akukumana ndi zokhoma makamaka kuchokera ku bungwe la zaumoyo padziko lonse la World Health Organization (WHO) lomwe limachenjeza za mchitidwe wosuta fodya.

Pa malonda a 2015, dziko la Malawi lidapeza ndalama zokwana K189 biliyoni kuchoka pa K205 biliyoni mmalonda a mchaka cha 2014.

Related Articles

Back to top button