‘Tidadziwana tili ana’

Mtolankhani wa za masewero ku wailesi ya Voice of Livingstonia (VOL) Sylvester Siloh Kapondera adakumana ndi wokondedwa wake Annie  Chivunga Kalasa ali ana m’boma la Kasungu.

Apatu n’kuti Kapondera ali ndi zaka 11, m’chaka cha 2001, ndipo ankacheza ndi achimwene a namwali wakeyu. Panthawiyo n’kuti Kalasa naye ali wachichepere kwambiri.

Ubwenzi wa anawatu udali bwino kwambiri chifukwa nawo makolo awo adali anansi pomwe onse ankaphunzitsa pa sukulu ya Mwimba, m’boma la Kasungu.

Siloh ndi Annisha: Zidayamba ngati chibwana

Koma patadutsa zaka zingapo anthuwa adatayana pomwe adalowera malo osiyana.

“Koma mudali m’chaka cha 2013 pomwe ndinkagwira ntchito kuwailesi ya Tigabane pomwe ndidayamba kumufuna namwaliyu! Panthawiyo n’kuti akuchita maphunziro ake auphunzitsi ku Nkhamenya,  m’boma la Kasungu,” adalongosola Kapondera.

Iye adalongosola kuti atamuona Kalasa mtima wake udatumphatumpha mpaka kupempha nambala yake ya lamya yomwe adapatsidwa mosavuta chifukwa adali kale anansi.

“Nditabwerera ku Mzuzu ndidayamba kuchezetsa ndipo ndidamuuza mawu a chikondi komabe ndidakanidwa, ndidayesetsa koma zidavuta! Kenako kukhala ndekha kudandivuta ndipo ndidapeza mkazi wina! Komabe mtima wanga umakumbukirabe Annie!” adatero Kapondera.

Koma mwatsoka adasiyana ndi mkazi winayo ndipo Kapondera sadaupeze koma kubwerera kwa Kalasa komwe mtima wake udali.

“Nditasiyana ndi mkazi winayo kumayambirilo kwa 2017 sindidachedwe kupitaso kwa Kalasa komwe malingaliro anga adali! Apaso nayeso sadachedwe koma kundisekerera nkundilora ataona zoti sindimafuna kupanga naye chibwenzi wamba koma ubwezi woti timange banja,” adalongosola Kapondera.

Komatu ubwenzi wa awiriwa wakumana ndi zokhoma zosiyanasiyana monga kupekeredwa nkhani mwa zina.

“Chomwe chidandikopa kwambiri kwaiye ndichoti kupatula kuwala kwa namwaliyo, Ali ndi khalidwe lwabwino, ndi ofatsa komaso okonda kuseka moti sindimavutika kupeze nkhani yoseketsa kwambiri kuti mwina ndioneko mano ake,” adatero Kapondera.

Iye adati chikondi chawo chimalimba chifukwa chokhulupilirana komaso kulemekezana ndi kumvetsetsana!

Polankhulapo, Kalasa adati adamukonda Kapondera chifukwa ankamuonetsera chikondi.

Kalasa adati Kapondera amakondedwa ngakhale  ndi abale ake.

Ukwati wa awiriwa uliko pa  April 28 kuholo ya sukulu ya sekondale ya Katoto.

Kapondera  ndi mwana wachiwiri kubadwa m’banja la ana asanu pomwe  Kalasa ndi mzime m’banja la ana 6.

Onsewa amachokera kwa Kaluluma m’boma la Kasungu. n

Share This Post