Chichewa

‘Tidagwirizira ukwati wa mnzathu’

Listen to this article

 

Akuti wokaona nyanja adakaona ndi mvuu zomwe. Naye wokagwirizira ukwati wa mnzake, adakapezako banja.

Izitu zikupherezera pa wolemba nkhani wa Times Group ku Mzuzu, Sam Kalimira, yemwe adakumana ndi bwenzi lake Chisomo Makupe pogwirizira ukwati wa mnzawo.

Awiriwa adavinira limodzi paukwatiwo.

Udali mwezi wa August, m’chaka cha 2014, pomwe Kalimira adamuona koyamba Chisomo patchalitchi cha CCAP cha Mchengautuwa mumzinda wa Mzuzu.

Monga achitira atsikana ambiri, Chisomo adali pakagulu ka atsikana anzake. Chisomoyutu adali atachokera ku Lilongwe komwe amakhala kudzagwirizira ukwatiwu.

Ngakhale akuti adalibe maganizo omufunsira, koma pansi pamtima adayamikira ndithu kuti namwaliyu ndi mkazi wabwino.

Ndikulonjeza: Sam kuveka mphete Chisomo  patsiku la chinkhoswe chawo
Ndikulonjeza: Sam kuveka mphete Chisomo
patsiku la chinkhoswe chawo

“Nditangomuona, mumtima mwanga ndidadziuza kuti namwaliyu ndi mkazi wabwino ngakhale ndidalibe ganizo loti ndingamufunsire ndipo tsiku lina n’kudzaganiza zomanga naye banja,” adatero Sam.

Mwina tingati, mtima wa mnyamayu sudasunthe kwenikweni chifukwa panthawiyo adali ali ndi bwenzi lina lomwe ankalifera.

Koma poti mtima wa mnzako ndi tsidya lina, ubwenziwu udatha ndipo Sam adakhala kwa miyezi yokwana  8 opanda bwenzi.

Apatu adali akulingalira zina ndi zina za moyo maka pankhani zachikondi. Monga mukudziwa kuti nkhani zachikondi ndi zovuta.

“Ndidayambanso kulingalira zopeza mkazi womanga naye banja, ndipo mwachisomo cha Mulungu maganizo a Chisomo adandibwerera,” adatero Kalimira.

Apa ndi pomwe mwana wam’muna nzeru zidamuthera chifukwa adali atapanga ubale wa pachilongo ndi Chisomo.

Kalimira adalongosolera Msangulutso kuti awiriwa ankaitanana kuti achimwene ndi achemwali.

Komabe monga mphongo, Sam adachita zotheka kuthetsa zachilongozo ndi kumufunsira namwaliyo.

Tsoka ilo, adakanidwa.

“Komabe nditayesayesa mwawi adandilola ndipo chibwenzi chidayamba mwezi wa August 2015,” adalongosola motero Kalimira.

Awiriwa sadachedwetsenso koma kupangiratu mwambo wa chinkhonswe n’kuyamba kukonzekera zomanga banja.

Ukwatiwu akaudalitsa pa 10 September 2016 ku Masintha CCAP ku Lilongwe ndipo madzulo ake anthu akakhwasula ku Bobo’s Residence ku 6 miles mumzinda womwewo. n

Related Articles

Back to top button