Chichewa

Tidziwane ndi Enock Balakasi wa Joy Radio

Listen to this article

Atolankhani m’dziko muno amakumana ndi zokhoma zambiri makamaka pofuna zoti auze mtundu wa Amalawi. Mwa zifukwa zina, kusoweka kwa lamulo lothandiza kuti atolankhaniwa azitha kutola nkhani paliponse popanda chowapinga ndi nkhani yomwe pakalipano ili mkamwamkamwa. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Enock Balakasi wa kanema ndi wayilesi ya Joy pankhaniyi.

Balakasi: Ufulu wolemba uli papepala basi
Balakasi: Ufulu wolemba uli papepala basi

Dzina lako ndani mbale?

Dzina langa ndi Enock Balakasi, wachiwiri m’banja la ana 7. Ndimachokera m’mudzi mwa Matandika kwa T/A Nkula m’boma la Machinga. Pano ndimayang’anira ofesi ya Lilongwe ya kanema ndi wayilesi ya Joy koma ndidalembedwa ntchito ngati mkonzi ndi mtolankhani.

Udayamba liti za utolankhani?

Utolankhani ndidauyamba mu 2007 nditamaliza maphunziro anga kusukulu yophunzitsa ntchito ya Blantyre Business College. Yemwe adandilimbikitsa kuti nditsatire za utolankhani ndi malume anga a Dr Rodrick Mulonya ndipo pano ndikupitirizabe maphunziro a zautolankhani chifukwa sindidafike pomwe ndimafuna.

Zimaonekatu ngati atolankhani m’dziko muno amavutika kuti apeze nkhani, kodi vuto n’chiyani?

Choyamba ndivomereze kuti ufulu wolankhula ndi kulemba ulipo koma kandodo kokwapulira kamakhala m’khundu. Ufuluwu umaoneka kuti uli papepala basi koma kuti ukwaniritsidwe pamavuta. Mwachitsanzo chabe, atolankhani akhala akugubuduka kupempha kuti pakhale lamulo lowapatsa mphamvu zogogoda khomo lililonse kukatola nkhani, lija amati Access to Information (ATI) koma zikuoneka kuti akuluakulu ena ali ndi maganizo ena pankhani imeneyi. Lamuloli litangotheka, zonse zikhoza kusintha n’kumayenda bwino pantchito ya utolankhani.

Nkani ina ndiyakuti nthawi zambiri m’dziko muno pamatenga nthawi kuti chomwe chachitika chimveke monga momwe maiko a anzathu amachitira, pamenepanso ndi nkhani ya lamulo lomweli?

Mbali ina tikhoza kunena kuti lamuloli limatengapo gawo lake koma kwakukulu ndi kusowa kwa zipangizo. Nyumba zambiri zoulutsa ndi kusindikiza nkhani muno mu Malawi zilibe zipangizo zokwanira ngati momwe makampani akunja mukunenawo. Mwachitsanzo, kuno kwathu pakakhala zochitika, nthawi zambiri timadalira omwe akonza zochitikazo kuti anyamule atolankhani komwe kuli kulakwitsa chifukwa pamenepo mumakhala kuti mwayamba kale kugwa mbali ya okutenganiwo. Njira yabwino ikadakhala yoti makampani oulutsa ndi kusindikiza nkhani akhale ndi zipangizo zawozawo kuti akafuna kukatola nkhani asamakhale ndi mbali ina iliyonse.

Nanga ubale wa ntchito ya utolankhani ndi andale umawuona bwanji?

Imeneyiso ndiye nkhani yomvetsa chisoni kwambiri chifukwa nthawi zambiri, anthu andale amatenga mtolankhani ngati chida chofuna kuwagwetsa pomwe mtolankhani amafuna kuti pomwe palakwika padziwike kuti ena akonzepo komanso pomwe pakhozeka padziwike kuti enanso atengereko phunziro kuti zinthu ziziyenda bwino. Chodandaulitsa kwambiri n’chakuti andale amangofuna atolankhani azilemba zabwino zokhazokha za iwo mpaka ena amafika pofuna kugula atolankhani. N’zomvetsa chisoni zedi. n

Related Articles

Back to top button
Translate »