Chichewa

Tinkakhala nyumba zoyandikana’

 

Mwayi wa banja umapezeka malo osiyanasiyana. Ena amapeza womanga naye banja mubasi, eetu paulendo, pomwe ena amakumana kutchalitchi. Koma kwa mphunzitsi wa sukulu ya utolankhani ya Malawi Institute of Journalism (MIJ) Jonathan Jere, sadathenso mtunda, koma adapeza m’khonde basi.

Pano Constance Kumwenda akutaya madzi pakhomo la Jere. Awiriwa adakwatirana chaka chathachi pa 5 December ku Mchengautuwa  CCAP ndipo madyerero adachitikira ku hotelo ya Chenda, mumzinda wa Mzuzu.

Komatu si kuti Jere adayenda mofewa kuti apeze mkaziyu poti adali woyandikana nyumba, ayi ndithu. Mwana wam’muna adakhetsera thukuta.

Jonathan ndi Constance patsiku lomwe adamanga woyera
Jonathan ndi Constance patsiku lomwe adamanga woyera

“Ndimakhala moyandikana nyumba ndi makolo ake ku Chiwavi. Ndipo maso anga adayamba kudyerera pa iye patatha ingapo,” adatero Jere.

Iye adati kwa miyezi 6 awiriwa sankacheza koma amangoonana ngati oyandikana nyumba.

Malinga ndi Jere,  namwaliyu  ndi namwino kuchipatala cha Mzuzu Central.

Pang’onopang’ono adayamba kumufufuza ndipo atamva zoti palibenso tambala wina yemwe amazungulirazungulira kholali, adalimba mtima.

Apatu Jere adafufuza nambala yake ya foni kuchokera kwa anthu ena ndipo adaipeza.

Apa awiriwa adayamba kulumikizana ndipo posakhalitsa Jere adapempha kuti akakumane poduka mphepo ndi kukambitsana ziwiri, zitatu.

Komatu izi sizidatheke chifukwa namwaliyu adakanitsitsa kuti nthawi yokumana ndi Jere adalibe.

“Ankati popeza tidali oyandikana nyumba anthu aziyesa zachibwana,” adatero Jere.

Naye Jere sadagwe ulesi koma adayesayesabe mwayi wake, mpaka tsiku lina adangoti naye gululu! Sadachedwenso koma kumuuza zakukhosi kwake.

“Pang’onopang’ono ndidayamba kubooleza mpaka chibwenzi chidayamba ndithu, koma padatha mwezi ndikugubira ndithu,” adatero Jere.

Iye adati polemekeza makolo komanso kuti kucheza kwawo kuziyenda bwino, adasamuka ndi kupeza nyumba ina kudera lina.

Adaonjezeranso kuti apa sadachitenso za bobobo, koma kuyamba kukonzekera za ukwati.

Koma popeza zokhoma sizilephera pa moyo, zinthu zidavuta kaamba ka mpingo.

“Anthu ena sadafune kuti atuluke mpingo wake ndi kulowa wanga. Komabe pa uwiri wathu tidakambirana ndi kugwirizana kuti alowa mpingo wathu,” adatero Jere.

Pakadali pano awiriwa akukhala mosangalala mumzinda wa Mzuzu. n

Related Articles

Back to top button