Chichewa

‘Tinkapita kumpira wa Silver’

Listen to this article

 

Ena akangomva za masewero ampira amalingalira zogenda, kuvala ziyangoyango kapena kuimba nyimbo basi komatu monga zochitika zina zilizonse, iyi ndi nthawi yokumana ndi anthu osiyanasiyana okonda zinthu ndi zochita zosiyanasiyananso.

Onse amakonda timu ya Silver: Daniel
Onse amakonda timu ya Silver: Daniel

Kudzera mumtendere woterewu, ena amachita mwayi waukulu pamoyo wawo mwina mpaka kupeza nthiti yawo monga momwe zidakhalira ndi Daniel Nthala wa m’mudzi mwa Yesaya, kwa mfumu yaikulu Kalumbu ku Kamphata m’boma la Lilongwe ndi Mary Kaliati.

Awiriwa akuti adakumana ali pasukulu ya Nkhoma pomwe onse ankaphunzira ndipo apa adali paulendo wopita kukaonerera masewero a timu ya Silver Strikers ndipo mwamwayi zidachitika kuti onse ankasapota timu yomweyo.

“Ine ndinkapita kukaonerera mpira ndiye patsogolo panga ndidaona munthu akulowera njira yomweyo. Pokhala munthu woti ndinkamuona pasukulu, ndidamuthamangira ndipo nditamufunsa komwe ankapita adandiyankha kuti adali paulendo wa kumpira,” adatero Daniel.

Iye adati apo awiriwo adayendera limodzi ndipo ali m’njira atazindikira kuti onse amakonda timu imodzi ubale udayambika pomwepo moti ankatengana nthawi zonse kukakhala mpira kukaonerera limodzi.

“Nditaona chidwi chake pampira komanso nditakhutira kuti zokonda zake ndi zanga ndi zofanana ndidaona chanzeru kuti tidzasungane ndipo nditamuuza, adagwirizana ndi maganizo anga,”adatero Daniel.

Mary adati iye ataona zomwe Daniel amakonda sadachotsere kuti adakumana ndi munthu yemwe angadzasungane naye popanda mavuto ndipo mwamaganizo akewo zidayendadi choncho mpaka pano akukhala limodzi ngati banja mokondwa.

“Zidangokhala ngati kuti ndife mapasa chifukwa zambiri zomwe ndimakonda, nayenso amakonda zomwezo monga kuleza ntima, khama pa zinthu ndi kukonda masewero ampira komanso timu yathu kukhala imodzi ndi chinthu chondisangalatsa kwambiri,” adatero Mary.

Awiriwa adamaliza zilinganizo zonse zoti anthu nkutengana ngati bambo ndi mayi ndipo pano ndi banja la ana atatu ndipo akuti anawonso akuyenda m’mapazi mwa makolo kukonda timu ya Silver Strikers.

Chikondi chomwe awiriwa ali nacho pa timu yomwe amasapotayi nchodabwitsa chifukwa akuti timuyi ikapanda kuchita bwino ngakhale chakudya onse awiri sachifuna mpaka kumatheka kugona nayo chakudya akuchiona.

“Timu ya Silver ikapanda kuchita bwino, kumatheka kungophika chakudya cha ana basi chifukwa kuphika chambiri tonse awiri sitidya chimagona ndiye tidazolowerana kuti momwe zakhaliramu titere,” adatero Mary. n

Related Articles

Back to top button