Nkhani

‘Tipulumutseni ku ukwati wa ana’

Listen to this article

Amati ana ndi tsogolo la mawa. Koma zikuchitika ku Neno zikukaikitsa ngati adzakhaledi atsogoleri mawa.

Kumeneko ukwati wa ana akuti wafika pa lekaleka ndipo ngati boma ndi mabungwe sachitapo kanthu, zinthu zifika poipitsitsa.

Lachinayi sabata yatha bungwe la Save the Children lidaitanitsa Nyumba ya Malamulo ya ana komwe anawa adatula nkhawa zawo kwa atsogoleri. Nyumbayo idakumana masiku awiri—Lachinayi mpaka Lachisanu.

Momwe zimachitikira sizimasiyana ndi momwe imakhalira Nyumba ya Malamulo ya dziko lino chifukwa mudali sipikala komanso aphungu.

Zonsezi zimachitika ndi ana am’boma la Neno amene amachokera m’sukulu zosiyanasiyana za m’bomalo.

Malinga ndi mlangizi wa ana ku bungweli, Thandizolathu Kadzamira, anawa adachita kusankhana kuti apeze owayimira pa sukulu yawo.

“Amasankha phungu wawo amene akawalankhulire m’nyumbayi ikamakumana. Adasankhanso sipikala wawo. Awatu ndi masukulu ambiri a m’boma lino,” adatero Kadzamira.

M’nyumbayi, anawa adalankhula Chingerezi ndi Chichewa osachita mantha ngakhale holo ya Neno idakhoma ndi anthu ofuna kudzaonera nkhumanoyo.

Nkhani zidamanga nthenje m’nyumbayi zidali zodandaulira boma komanso mabungwe kuti awapulumutse ku maukwati a ana omwe akolera m’bomalo.

Anawa adapemphanso kuti boma liwamangire sukulu zabwino ndi kuikamo zipangizo zoyenera.

Sipikala wa nyumbayo, Trifonia Kaduya, wa zaka 14 ndipo akukalowa folomu 2 pa sekondale ya Chiwale, adati akuluakulu asiye kuimba nyimbo ndipo ayambe kuchita.

“Timalankhula koma palibe chimachitika. Nkhumano ino tikufuna akuluakulu athu ayambe kuchita,” adatero.

“Mwana wa zaka 14 umupeza wakwatiwa kale. Kodi apa palinso lonjezo loti mawa tidzakhala atsogoleri?” adadabwa sipikalayu.

Wotsogolera komiti yokhudza ana ku Nyumba ya Malamulo, Richard Chimwendo Banda, adalonjeza sipikala Kaduya kuti nkhawa zawo ziyankhidwa.

“Alankhula mopanda mantha. Izi ndi zomwe tikufuna kuti zithandizire chidwi chathu chofuna kuthandiza ana. Amve kwa ine kuti tichitapo kanthu,” adatero Banda.

Iye adati Nyumba ya Malamulo ya dziko lino ikamakumana adzatenga ena mwa anawa kuti akalankhule kunyumbayi cholinga aphungu akadzimvere mavuto amene anawa akukumana nawo.

Related Articles

Back to top button
Translate »