Titsirika nkhalango zonse—Ng’anga

Gulu lina la asing’anga ku Dedza ladzithemba kuti likhoza kuteteza nkhalango za dziko lino ndi chambu koma akuluakulu a boma ati zonse zili m’manja mwa asing’angawo kuti awakhutitse kuti njirayo idzayenda.

Mkulu woyang’anira za nkhalango m’dziko muno Clement Chilima adati nthambiyo ndi yokonzeka kupereka mpata kwa asing’angawo kugwira ntchito ndi asing’angawo poteteza nkhalangozo.

Kodi nsupa ndi zitsamba zingathandize kuteteza nkhalango?

Iye adati chomwe asing’angawa angachite n’kulembera kalata nthambiyo kuti ifunse upangiri pena ndi pena koma ganizo lawolo ndi lolandiridwa ngati silikuphwanya malamulo.

“M’magwiridwe a ntchito yathu, timalandira aliyense yemwe ali ndi njira yothandiza. Ngati asing’angawa akunena zoona ndipo njira yawoyo siyikuphwanya malamulo, abwere tiwapatsa mpata,” adatero Chilima.

Mkulu wa nthambi yoteteza nyama za kutchire Brighton Kumchedwa adati sanganeneretu mwa ndithendithe kuti chambu ndiye yankho koma adati gulu la asing’angalo ndilolandiridwa ngati likudziwadi njira yomwe ingathandize kuteteza nkhalango.

“Ntchito yathu ndi yogwira ndi anthu ndiye ngati papezeka ena omwe akuti ali ndi njira yomwe ingathandize, chowaletsera n’chiyani? Atatipeza n’kutifotokozera bwinobwino, ndipo titamvetsa, tikhoza kuona kuti tingagwire nawo bwanji ntchito,” adatero Kumchedwa.

Iye adati m’dziko muno muli nkhalango 84 zomwe zimafunika chitetezo chifukwa mitengo ndi nyama zopezeka mmenemo zikutha mosakhala bwino chifukwa cha mbala.

Gulu la asing’angali ndi lochokera m’boma la Dedza ndipo lanenetsa kuti chambu chikhoza kugwira ntchito yoteteza nkhalango kuposa ntchito ya alonda ndi asilikali.

Nthambi ya za nkhalango ndi nyama zopezeka mmenemo, itaima mutu ndi mchitidwe opha nyama komanso kudula mitengo mozemba, idalemba alonda omwe amathandizana ndi asilikali kuteteza nkhalango ndi nyama.

Woyang’anira ndi kulangiza asing’anga pantchito yawo m’boma la Dedza, Gulupu Ntambeni Chinyamula adati kupatula chidima, ophotchola m’nkhalango akhoza kukakamiraa mpaka kugwidwa momwemo.

“Chambu n’champhamvu zedi chikhoza kugwira munthu yemwe amafuna kukasokoneza m’nkhalango mpaka kugwidwa momwemo n’kulandira chilango choyenera,” adatero Chinyamula.

Pulezidenti wa asing’anga a mdziko muno Frank Manyowa adati n’zotheka kuteteza nkhalangozi potsirika nkhalangozo ndi chambu mmalo modalira alonda ndi asilikali.

“Ndi chambu, tikhoza kuteteza nkhalango zonse zomwe zikusowa chitetezo kuti owonongawo asamazione powakantha ndi chidima ndipo akhoza kulephera kupanga upandu omwe adakonzawo,” adatero Manyowa.

Iye adati asing’anga ali ndi njira zambiri zomwe akhonza kulangira anthu oononga nkhalango ndipo zilangozo zikhoza kuwapatsa mantha moti sangalakelake kubwerera kunkhalango.

Manyowa adati asing’anga zimawapweteka nkhalango zikamaonongeka chifukwa kasupe wa ntchito yawo wagona mmenemo.

“Timalimbikitsa kuteteza nkhalango chifukwa ndiko timapeza mankhwala athu. Boma lakhala likuyesetsa kuteteza nkhalango koma zikuwoneka kuti zikuvuta koma asing’anga akhoza kukwanitsa ndi chambu,” iye adatero.

Share This Post