Chichewa

Tsabola ndi waphindu, wophweka kulima

 

Ulimi wa tsabola umaoneka opanda pake komanso ogwetsa mphwayi, koma Benison Kuziona, mkulu wa Bungwe la Zikometso Innovation and Productivity Centre akuti ulimiwu ndi waphindu komanso wophweka.

Kuziona adati ndi ndalama yochepa, mlimi amatulutsa ndalama zochuluka. “Chaka chathachi, mbewuyi idafika pamtengo wa K3 000 pa kilogalamu ndipo alimi omwe adalima, adachita nayo mphumi kwambiri,” adatero mkuluyu.

Iye adaonjezanso kuti ubwino wina wa tsabola ndi woti ukabzala chaka choyamba, chaka chachiwiri subzalanso chifukwa mvula ikangogwa mitengo ija imaphukiranso ndipo zokolola zake zimakhala zochuluka kuposa poyamba.

Tsabola ndi mbewu imene alimi ena akupindula nayo kwambiri

 

A  bungwe la Malawi Fruits mogwirizana ndi Mzuzu Agriculture Development Division (Mzadd) adachita kafukufuku wa tsabola m’zaka za mmbuyomu ndipo adapeza kuti kulima tsabola ndi kophweka komanso sikulira ndalama zochuluka poyerekeza ndi mbewu zina.

Ngakhale izi zili chomwechi, president wa bungwe la Farmers Union of Malawi, Alfred Kapichira Banda, wati alimi ena atsabola m’madera ena  m’dziko muno amagulitsa kwa mavenda pamtengo wotsika kwambiri. Iye adati alimi ambiri  sakudziwa misika yeniyeni ya tsabola kotero amangoberedwa ndi mavenda.

“Tikupempha misika yovomerezeka yomwe imagula tsabolayu kuti ibwere poyera, tikufuna alimiwa azitha kugulitsa pa mitengo yabwino,” adatero Kapichira Banda.

Iye adati chifukwa chakuti alimiwa akhala akugulitsa pa mitengo yotsika, ambiri akumangolima moyerekeza pomwe ena adalekeratu ulimiwu.

Bungwe la Zikometso Innovation and Productivity Centre ndi limodzi mwa mabungwe omwe amalimbikitsa za ulimi wa tsabola. Zikometso, ndi nthambi ya bungwe la National Smallholder Farmers Association of Malawi (Nasfam).

Ntchito zake ndi kugula tsabola kwa alimi, kuwagulitsa njere zabwino komanso kuwaphunzitsa momwe angalimire tsabolayu kuti azikolola ochuluka komanso wapamwamba. Bungweli lili ndi fakitale yomwe imapanga tsabola wa m’mabotolo yemwe amagulitsidwa m’Malawi ngakhalenso maiko akunja.

Malinga ndi Kuziona, ulimi wa tsabola umayambira ku nazale ngati momwe anthu amachitira ndi ulimi wa mbewu za masamba monga tomato. “Tsabola amayenera kufesedwa kumapeto kwa mwezi wa October ndipo akuyenera kuwokeredwa pamene mvula yayamba kugwa yochuluka,” adatero Kuziona.

Iye adafotokoza kuti mizere imayenera kutalikana masentimita 75 komanso pobzala, mapando amayenera kutalikirana ndi masentimita 45.

“Akayamba kuphukira, amayenera kudulidwa tisonga take kuti apange nthambi zochuluka. Izi zimathandiza kuti pamtengo uliwonse mlimi adzakolole tsabola ochuluka,” adatero Kuziona.

Iye adaonjezanso kuti mbewuyi imayenera kuthiridwa feteleza wa D Compound ikangobzalidwa kumene komanso CAN pakadutsa masiku 21.

“Kathiridwe kake ndi kofanana ndi momwe timathirira ku chimanga. Fetelezayu amathandiza tsabola kuti akule bwino komanso abereke mochuluka,” adatero mkuluyu.

Iye adaonjezanso kuti tsabolayu nthawi zina amatha kugwidwa ndi matenda komanso tizilombo.

Tizilombo tomwe timasakaza mbewuyi ndi tofanana ndi tomwe timagwira mbewu za mtundu wa masamba monga tomato ndipo mankhwala ake ndi ofanana ndi omwe amapoperedwa kumbewuzi. “Mlimi akhonza kupopera mankhwala koma chachikulu ndi kubzala mbewu zabwino komanso kumapalira kuti apewe matenda ndi tizilomboti,” adatero Kuziona.

Iye adafotokozanso kuti tsabola amachita bwino kwambiri ku madera osazizira komanso osatentha kwambiri ndipo amafuna dothi losakanikirana bwino. n

Related Articles

Back to top button