Nkhani

TUM imemeza sitalaka ya aphunzitsi lolemba

Listen to this article

…Makolo, katswiri apempha boma lichitepo kanthu

Sukulu za boma za pulayimale ndi sekondale m’dziko muno zikuyembekezereka kuima kuyambira mkucha Lolemba ngati aphunzitsi angayambedi sitalaka pofuna kukakamiza  boma kuti liyankhe madandaulo awo.

Akufuna zawo: Aphunzitsi kunyanyala ntchito mmbuyomu
Akufuna zawo: Aphunzitsi kunyanyala ntchito mmbuyomu

Chikalata chomwe bungwe la aphunzitsi la Teachers Union of Malawi (TUM) lalembera boma ndi nthambi zosiyanasiyana chati aphunzitsi onse m’sukulu za boma za pulayimale ndi sekondale ayamba kunyanyala ntchito mkucha uno ngati boma silipereka yankho logwira mtima pa madandaulo omwe bungweli lidapereka kuboma.

Mtsogoleri wa bungwe la TUM Chauluka Muwake adati mwa madandaulowa, undunawu udangoperekako ndalama zokapumira kusiya mavuto enawo osayankhidwa mogwira mtima.

Bungwe la TUM lidapereka madandaulo 24 ku unduna wa zamaphunziro ndipo ena mwa iwo ndi kutsitsa aphunzitsi omwe adakwenzedwa pantchito; kulephera kuonjezera malipiro aphunzitsi omwe adakwenzedwa m’chaka cha 2013; kulephera kulipira aphunzitsi a m’sukulu za sekondale ndalama zomwe amayenera kulandira pokapuma; komanso kulephera kulipira aphunzitsi a kupulayimale ndalama zamgonagona.

Nkhaniyi yakhudza makolo omwe ali ndi ana m’sukuluzi ndipo katswiri pa zamaphunziro, Benedicto Kondowe, wati nkhaniyi yafika apa kaamba ka kulephera kwa unduna wa zamaphunziro kupereka chilimbikitso kwa aphunzitsi.

Kondowe wati ngakhale malipiro a aphunzitsi ali ochepa, boma litamawalipira munthawi yake ndi kuwapangira zinthu zina zing’onozing’ono moyenera, aphunzitsiwa akhoza kukhala ndi chilimbikitso pantchito yawo.

Iye adati ndondomeko ya maphunziro m’dziko muno ndi yothinana mwakuti kuimitsa maphunziro ndi sabata imodzi kapena ziwiri ndi nkhani yoopsa kwambiri pamaphunziro kwa makolo, ophunzira ndi aphunzitsi.

“Choyamba, kukakhala sitalaka, sukulu zambiri zimabweza ana kuopa zipolowe. Pamenepa muganizire makolo kumbali ya ndalama zoyendera ndi zina zomwe adali atagula kale.

“Kwa ana, n’chosokoneza kuyamba kuwaphunzitsa kenako aime chifukwa ena amavutika kutolera zinthu msanga. Kwa mphunzitsi, ntchito yomwe akadapanga pasabata ziwiri ndi yambiri ndiye pofuna kuti agwirane ndi ndondomko, amaphunzitsa mongowaula ana bola amalize,” adatero Kondowe.

Lameck Majawa, kholo lomwe lidalankhula ndi Tamvani Lachiwiri bungwe la TUM litatsimikiza za sitalakayi, adati boma likadagonjera aphunzitsi n’kuwapatsa zofuna zawo kuti sitalakayi isachitike ndipo mavuto omwe angadze ndi sitalakayi apeweke.

Iye adati maphunziro akulowabe pansi chifukwa ngakhale popanga ndondomeko ya chuma cha dziko lino unduna wa zamaphunziro umaganiziridwa ngati umodzi mwa maunduna omwe amapatsidwa ndalama zambiri.

“Izi si zoona, ayi, nthawi ndi nthawi tizimva nkhani imodzimodzi popanda kupanga njira zothetsera mavuto amenewa? Tatopa nazo izi, aganizepo bwino ndi kupangapo kanthu kuti sitalakayi isachitike,” adatero Majawa.

Kholo lina, Grace Chawinga, adagwirizana ndi Majawa kuti njira ndi imodzi yokhayo yopereka zomwe aphunzitsi akufuna boma liwachitire kusiyana n’kumakokanakokana, zomwe adati n’kuphwanya ufulu wa ana olandira maphunziro apamwamba.

TUM yapereka kalata yake ku ofesi ya mlembi wamkulu wa boma, mlembi wa nthambi yopereka ndalama za boma, mlembi wa unduna wa zantchito, kubungwe la Maneb, nthambi yoyang’anira ntchito ya uphunzitsi, likulu la mabungwe a anthu apantchito ndi kumaofesi oyang’anira za maphunziro m’maboma.

Mkalatayi, TUM yati aphunzitsi onse m’sukulu za boma za sekondale ndi pulayimale ayamba kunyanyala ntchito Lolemba ngati boma silipereka yankho logwira mtima pa madandaulo omwe bungweli lidapereka kuboma.

Mneneri wa unduna wa zamaphunziro Manfred Ndovie adauza nyuzipepala ya The Nation kuti undunawu sungakwanitse kuthana ndi zonse zomwe aphunzitsiwa akufuna koma pang’onopang’ono.

Adanena izi zokambirana zomwe zidaliko pakati pa bungwe la TUM ndi nthumwi za boma kuyambira Lachinayi sabata yatha zisadachitike ndipo pamapeto pa zokambiranazo, TUM idati boma silidawayankhe momveka bwino ndipo pachifukwachi sitalaka ikhalapo baso.

Zokambiranazi zitatha, Muwake adauza nyuzipepala ya The Nation kuti boma lili ndi ndalama za aphunzitsi zokwana K1.4 biliyoni zoyang’anirira mayeso a MSCE omwe sadatuluke; K246 miliyoni za aphunzitsi omwe adakwenzedwa koma samalandira molingana ndi giredi yawo; komanso K103 miliyoni za aphunzitsi opuma ndi omwe adamwalira.

Kondowe adati ngakhale nkhaniyi ndi yobwezeretsa maphunziro mmbuyo, aphunzitsi ali ndi mfundo zokwanira zochitira sitalaka kaamba koti nthawi zambiri boma siliika chidwi pa mavuto awo.

Pachiyambi, TUM idakonza zoyamba sitalaka Lolemba lathali tsiku lotsegulira sukulu koma zidalephereka chifukwa aphunzitsi adati adali asadalandire chidziwitso chenicheni ndipo sukulu zambiri aphunzitsi adaphunzitsa.

Related Articles

Back to top button