Nation Online

Saturday, May 18th

You are here: Home Uchikumbe

Nkhani

Alimi asamale ndi chitopa

Unduna wa Zamalimidwe muno m’Malawi wati chitopa ndi amodzi mwa matenda omwe amalowetsa pansi ulimi wa nkhuku ndipo wapempha alimi kuti azitsata njira zabwino kuti matendawa asagwire ziweto zawo.

Alimi agundika ndi mthirira

Mkulu wa nthambi ya zaulimi ku Lilongwe ADD, Hastings Yotamu, wati chiyambireni ntchito za ulimi wamthirira m’dziko muno ulimi ukupita patsogolo komanso alimi akupeza phindu lochuluka.

Yotamu wati alimi ambiri omwe amachita nawo ulimi wamthirira tsopano amapeza zokolola zopambana theka la zokolola zomwe amapeza nyengo ya ulimi wodalira mvula.

Ku Mulanje alimi anyadira sikimu

Alimi oposa 250 mwa T/A Nkhulambe m’boma la Mulanje akuyembekezera kusimba lokoma atalandira sikimu ya ulimi wamthirira yomwe apatsidwa ndi bungwe lolimbikitsa ulimi wamthirira la Irrigation Rural Livelihoods and Agriculture Development (Irlad).

Kufunika kwa zakudya za m’tchire

Papita zaka 2 500 kuchokera pamene wotchuka wina wodziwika ndi dzina loti Hippocrates adati: "Chakudya chikhale mankhwala anu komanso mankhwala akhale chakudya chanu".

Kutchisa bwino fodya ndi kofunika

Kutchisa fodya wa bale sikuyanika fodya padzuwa kuti aume. Kutchisa fodya ndi ntchito yofunika ukadaulo wapadera kusiyana ndi mmene ambiri amaganizira.

K16 biliyoni ya ulimi wa mthirira

Dziko lino likhoza kusandukanso nkhokwe ya zakudya m’dera lino la Afrika posachedwapa kaamba ka ndalama zankhaninkhani zomwe bungwe losunga ndi kubwereketsa ndalama za chitukuko muno mu Africa la African Development Bank (ADB) lapereka kudziko lino pothandiza kutukula ulimi wamthirira.

Adandaula za mankhwala

Alimi a thonje ena m’maboma a Balaka, Neno ndi Mwanza akhumudwa ndi momwe boma lagawira mankhwala a thonje chifukwa ena aperewedwa.

Ulimi wa chikole ukuthandiza

Ngakhale alimi ena akunyadira kuti njira yomwe makampani ogula fodya akugwiritsa ntchito yokongoza alimi zipangizo mwachikole ikuthandiza kutukula alimi ang’onoang’ono, alimi ena akuti njirayi sinafike pokhazikika, makamaka pankhani ya mitengo yomwe makampaniwa amagulira fodyayu komaso kadulidwe ka ndalama ya ngongole.

Alimi ayendera thonje la makono la Blantyre

Alimi ochokera m’zigawo zonse za dziko lino anakhamukira kusukulu ya ukachenjede ya Bunda College ku Lilongwe komwe anakadziwonela okha m’mene mbewu ya thonje la BT likukulira, pakadali pano mbewuyi yamasula maluwa.

Katakwe pankhani yazofufuza kusukuluyi, pulofesa Moses Kwapata ndiye akutsogolera ntchitoyi. Aka ndikoyamba mbiri ya ulimi m’dziko muno kuti Malawi adzale thonje lopangidwa musayansi ya BT.

Zakudya za odwala nthenda ya shuga

Mwezi wathawu udali wokumbukira matenda a shuga ndipo malingana ndi bungwe la anthu odwala matendawa, mwa anthu 20 alionse mmodzi amadwala matenda ashuga kusonyeza kuti nthendayi ikuchulukirabe.

Bungweli lidatinso n’kofunika kuti anthu odwala matendawa ayenera kumapanga masewero olimbitsa thupi komanso kudya zoyenera.