Nation Online

Thursday, May 23rd

You are here: Home Uchikumbe Kusanthula makuponi

Kusanthula makuponi

Njira yonena kuti magulupu ndi mafumu ena azipatsidwa tsiku loti iwo ndi anthu awo akagule zipangizo zotsika mtengo m’ndondomeko ya Farm input Subsidy Programme (FISP) ndi imodzi mwa zinthu zimene zidachititsa kuti ndondomekoyi iyende bwino chaka chatha.

Malinga ndi pulogalamu ya Kalondolondo imene yakhala ikufufuza momwe ndondomekoyi idaliri chaka chatha m’maboma ena a m’dziko muno kudapezeka kuti zovuta zambiri zomwe zidalipo mu 2011 pachilinganizochi zidathetsedwa.

 

Polankhula Kalondolondo atafukula momwe ndondomekoyi idayendera m’maboma ena kuphatikizapo Chikhwawa, Chiradzulu, Mwanza ndi Machinga, mkulu wa pulogalamuyo Jephter Mwanza adati nzosangalatsa kuti mavuto ena amene adaliko chaka chatha adatheratu ndipo ndondomekoyo yayenda bwino.

“M’mbuyomo kudali vuto la kusowa kwa zipangizo, apolisi ena amamenya molapitsa alimi pakakhala kulimbirana zipangizozo koma izi zidachepa chaka chatha, makamaka chifukwa mafumu amapatsidwa tsiku loti akagule fetereza limodzi ndi anthu awo. Izi zimachepetsa chipwirikiti komanso katangale wodza ndi chipwirikiticho,” adatero Mwanza.

Ndipo Mwanza adati ngakhale ntchitoyi idayenda, m’madera ena mudali vuto la nyakwawa zina zimene zimalemba ngakhale olemera ndipo nthawi zina amapereka maina a bodza.

“Chopatsa chidwi n’chakuti m’madera ena mafumu amaitanitsa anthu awo pamodzi ndipo amauza anthuwo asankhe omwe akuona kuti ndiwoyenera kulandira makuponi. Iyi ndi njira yabwino,” adatero Mwanza.

Limodzi mwa maboma amene adachita bwino chaka chino kuposa chaka chatha ndi la Mwanza, kumene anthu 80 mwa 100 adati zidayenda bwino kuyerekeza ndi 54 mwa 100 amene adavomereza chaka chatha.

Mkulu wa zaulimi m’bomalo Vincent Wandale adati mgwirizano pakati pa a zaulimi, apolisi, mafumu ndi anthu, udathandiza kuti zinthu ziyende.

Koma anthu ena kumeneko adati ngakhale zinthu zidayenda, padali zovuta zina monga katangale wa mafumu.

George Mazeze wa m’mudzi mwa STA Govati ku Thambani m’boma la Mwanza, nyakwawa zina zidabweza ma K500 kwa anthu amene adagula fetereza wotsika mtengo ndi kuwalanda fetereza.

“Vuto lalikulu ndi lakuti anthu amaopa mafumu ndiye adangolandidwa fetereza wogulawogula. Koma ena adalembera a T/A omwe adatithandiza,” adatero iye.

Malinga ndi T/A Nthache ya m’bomalo, ataona kuti nyakwawa zina ndizachinyengo adazichotsa.

“M’madera ena zidali zovuta kwambiri, mpaka nyakwawa zina zidali kutuma a gule wamkulu kuti akaopseze alimi ena,” adatero Nthache.

Ndipo Rhoda Mwale adati kusowa kwa zipangizo kudawakhudzanso. “Timachokera kutali ndipo tidasonkherana K70 000 yochitira hayala galimoto koma titapita kumsika adatiuza kuti zipangizo kulibe

Ndipo anthu ena amene tidacheza m’maboma ena, adatambasulanso ena mwa mavuto amene adakumana nayo pa chilinganizochi.

Ferista Malizani wa m’mudzi mwa Kavina kwa T/A Kadewere m’boma la Chiradzulu adati ndibwino boma lipeze njira ina yothandizira anthu ovutika pa fetereza chifukwa sadathe kugula fetereza wotsika mtengo ndipo mpaka pano akusunga makuponi.

“Makuponi ndiye tidalandira mosavuta koma fetereza amangotiuza kuti tilandira koma mpaka lero kuli zii. Mudzi onse palibe adakalandira, titafunsa adati tidikire koma mpaka lero chimanga chacha tikudikirabe,” adatero Malizani.

Nako ku Dedza kwa gulupu Lodzanyama akuti kwavuta. Monga ikufotokozerera mfumuyi, anthu a m’mudzi wake ndi ina yozungulira sadagule fetereza wotsika mtengoyu.

“Kufika lero ifenso tatopa ndipo sitikuwonanso kuti tingapeze feterezayu. Anthu anga onse sadalandire fetereza, takumanapo ndi akuluakulu omwe boma koma palibe chochitika, boma litiganizire chifukwa iyi ndi njala,” adatero Lodzanyama.

Add comment

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.


Security code
Refresh