Kusamalira tomato nkofunika
- Category: Mwatiyendera
- Written by Bobby Kabango
Nthawi ya mvula ikakwana, tomato amavuta kulima. Ngakhale m’misika amasowa. Koma ku Chiradzulu kuli alimi ena omwe ngakhale tili m’nyengo ya mvula, ulimi wa tomato ukuwayendera. BOBBY KABANGO adali komweko sabata yathayi ndipo adacheza nd mlimi mmodzi, Eladi Katsabola, wa m’mudzi mwa Masiku kwa T/A Mpama m’bomalo.
Tifotokozereni za ulimiwu kuyambira ku nazale..
Ulimi wa tomato ndi wovuta mukasiyanitsa ndi ulimi wina, vuto lalikulu ndi matenda omwe amagwira tomatoyu. Ndiye ndiloleni nditambasule za ulimiwu kuyambira panazale.
Masukani…
Choyamba timakonza mabedi ndiye timalemba moti tiwazemo njere za tomato panazalepo. Tikawaza njerezo ndiye timatenga mchenga ndi kuwazanso kuti njere zija zisamatirire ku dothi pomwe zikumera. Likakhala dothi, njere zimamatirira kusiyana ndi mchenga. Tili panazale pomwepo timawaza mankhwala a Dythen ndi Copa kuti tichotse chiwawu komanso masamba akhale obiriwira pomwe tikukonzekera kuti tichotse mbewuyo kupita nayo m’munda.
Ntchito yopita kumunda imakhala bwanji?
Choyamba timakakumba mapando ndiye m’mapandomo timathiramo manyowa. Atha kukhala manyowa a mtundu uliwonse koma paphandopo pakhale nthaka. Tikatero timawokera mbewu ija. Pomwe tawokera pakangotha masiku 7 timayenera kuthira fetereza. Cholinga n’kuti mtengo wathu wa tomato ukhale wa mphamvu kutinso abereke bwino.
Tafotokozani bwino za malo omwe tikuyenera kubzala tomato….
Mapando atalitalikane ndi phazi limodzi komanso theka. Akhale malo opanda miyala oti mtengo utha kumera bwino. Izi ndiye zimayenera kuchitika pomwe mukukonza za malo oti mubzalapo mbewu yanu.
Mukaoka, mumachitanso chiyani?
Timakhala tikusamalamo koma pakutha pa masiku 7 timathira mankhwala a Copa kuti masamba aja akhalebe obiriwira. Tsamba limakhala lokhuthala bwino ngati mukuthira bwino mankhwalawa. Pomwe mtengowo ukukula timayendera ndi kumapungula nthambi za mtengowo kuti udzabereke bwino komanso wamkulu. Kupungula nthambi kumayambika pomwe akuthamangira pochita maluwa.
Taona kuti mwamangira kampanda, cholinga n’chiyani?
Tomato akayamba kubereka amalemedwa komanso nthambi zomwe mwazisiya kuti zibereke zimayanga kuti zizipeza pokhala. Umu ndimo zimayangira komanso pomwe akubereka amakhala. Pomwe wayamba kubereka timathira fetereza wa CAN kuti abereke bwino.
Kodi mtengo wa tomato umakhala nthawi yaitali bwanji? Nanga ungabereke motani?
Mtengo wake umakhala miyezi itatu kapena inayi. Pofika panthawiyi mtengo umakhala wabereka mokwana. Mtengo umodzi ukabereka bwino utha kuchotsa kathumba ka makilogalamu 20.
Mvula ikamagwa chonchi inu mumadandaula, vuto limakhala pati?
Matenda amachuluka komanso kupopera kumafuna kuchitike mvula itadula, ndiye nthawi imeneyi sitipopera mankhwala moti apa tomato wambiri wawonongeka chifukwa cha mvulayi. Masiku atatu ena ake inadula ndiye tapopera, padakapanda apo ndiye zidakavuta.
Muganiza mukolola liti? Munda wanu ndiwokula bwanji?
Chiyembekezo n’kuti mwezi wa March tikhala tikukolola. Mundawu ukuposa kota ya ekala.
