Akulira ndi mitengo ya nyemba zaziwisi
- Category: Pansika
- Published Date
- Written by Steven Pembamoyo
Nyemba zaziwisi zayamba kufika kumsika tsopano koma ogulitsa ati sakupeza phindu lenileni ndi mitengo yomwe nyembazi zikugulitsidwira poyerekeza ndi ntchito yomwe inalipo kuti mpakana nyembazi zikapezeke pamsika.
Mmodzi mwa ogulitsa nyembazi mumsika waukulu ku Lilongwe Maxwel Thabi wati mitengo yomwe nyembazi zayambira ndiyotsika kwambiri komanso yogwetsa ulesi poyerekeza ndi mitengo yomwe mavenda akuluakulu amagulitsira akazisunga ndikudzagulitsa mtsogolo.
Thabi anati zikanakhala bwino mitengoyi ikanaunikidwa ndikusinthidwa kuti ochita malonda aang’onoang’ono nawo azipezapo phindu lokwanira.
“Timayembekezera mitengo yabwino kutengera mitengo yomwe mavenda anzathu amagulitsira nyemba zouma koma zinthu sizikutiyendera chifukwa ogula akulirira mitengo yotsika. Panopa jumbo imodzi ikugulitsidwa K500 pomwe mlingo ngati omwewo kuusenda ndikuyanika ukhoza kubweretsa ndalama zochulukirapo,” anatero Thabi.
Iye wati alimi ndiwo akumva kuwawa kwambiri chifukwa amalonda akulimbira mitengo yotsika kwambiri posawerengera ntchito yomwe alimiwo amagwira koma chifukwa choti msika omwe ukupezeka padakali pano ndiwamavenda omwewo alimiwo alibe chisankho chilichonse.
Thabi anati amalonda omwe akugulitsira mumsika padakali pano ndi amene akupezako phindu kusiyana ndiomwe akuyenda m’makomo chifukwa mitengo yawo imasinthasintha pofuna kugwirizana ndi owagula.
“Mwina zikanathandizako kukanakhala kuti onse ogulitsa akutha kupeza malo mumsika koma malowo akuchepa chifukwa malonda achuluka ndipo ambiri akusowa malo mapeto ake akumayenda ndi malonda awo m’malo omwe anthu amakhala mapeto ake zikuwavuta kukhala ndi mtengo okhazikika bwinobwino,” iye anatelo.
Oyendetsa ntchito zotukula ulimi m’boma la Lilongwe (DADO) Hastings Yotamu wati alimi ambiri amakakamizidwa kugulitsa mbewu zawo kwa ogula achinyengo chifukwa cha mavuto.
Iye anati pofuna kuthana ndi vutoli, boma likulimbikitsa alimi ang’onoang’ono kuti azikhala m’magulu ndikumagulitsira katundu wawo pamodzi kuti azipeza misika yabwino ndikumapanga phindu lochuluka.
“Pakali pano kudzera mumgwirizano wathu ndi mabungwe omwe siaboma tikuwamangira alimi omwe ali m’magulu nyumba zosungiramo zokolola zawo kuti akapanga gulu lawolo azisonkhanitsa zokolola zawo ndikusunga m’nyumbazi kuti adzagulitse pamitengo yabwino m’tsogolo,” anatero Yotamu.
