Ukatswiri wa Kaira pachikopa

August 11, 2013 • Nkhani • Written by :

Kaira: Makampani alowererepo

Kaira: Makampani alowererepo

Chimango Kaira ndi dolo komanso mtima wa timu ya Big Bullets ngakhalenso ku Flames. Kodi chinsisi cha Kaira chimatsamira pati? STEVEN PEMBAMOYO akucheza naye

 

Tafotokoza kaye za kumene umachokera.

Bambo anga kwawo ndi ku Nthalire ku Chitipa pomwe mayi anga kwawo ndi kwa Ntwalo ku Mzimba.

 

Udayamba liti kusewera mpira?

Ndidayamba kale ndithu ndili mwana koma kusewera zodziwika ndidayamba m’chaka cha 2006 ndili Folomu 3 nthawi imene timachita mpikisano wa chikho cha Coca Cola. Ndimakumbuka kuti nthawi imeneyi ndidasankhidwa kukasewera mutimu ya dziko lino mumpikisano omwewu ku Zimbabwe.

 

Udadziwika bwanji ku m’matimu akuluakulu?

Titachoka ku Zimbabwe komwe tidachita bwino kwambiri, timu ya Escom idanditenga kutimu yawo yaying’ono m’chaka cha 2007 komwe ndidakasewera magemu 6 kenako ndikundikwenza kuti ndiyambe kusewera mutimu yaikulu koma umu mudali mu 2008.

 

Ndichiyani chomwe umakumbukira ndi kunyadira pa mbiri yako ya mpira?

M’chaka cha 2009 ndikusewera mutimu yaikulu ya Escom tidamaliza chaka chonse osachinyidwako mumpikisano wa Super League. Ichi chidali chaka changa chonyaditsa kwambiri chifukwa ndipomwenso ndidayamba kusewera zenizeni m’moyo mwanga moti olo anzanga amene ndimasewera nawo panthawiyo amadziwa.

 

Wasewera matimu angati akuluakulu m’moyo wako?

Awiri basi nditachoka ku Escom United ndidapita ku timu ya Big Bullets m’chaka cha 2011.

 

Nanga udayamba liti kutengedwa mu timu yaikulu ya dziko lino?

Mudali mu 2010 nditavuta kwambiri. Ndimathokoza Mulungu ndi akuluakulu oyendetsa za mpira chifukwa kunena zoona nthawi imene ndimayambayo kudali anyamata osewera bwino mpira moti inenso ndimayamika chimenecho ndicho chidandipangitsa kuti ndilimbikire kwambiri.

 

Tandiuze mphunzitsi wa mpira yemwe umati ukawona umakumbukira zomwe adakuchitira?

Young Chimodzi ndi kusewera mu ya Escom. Iyeyu ndi amene adandikweza kuchoka mutimu yaing’ono kupita mu timu yaikulu nditangosewerako magemu 6 basi komanso ankandilimbikitsa pa zochita zokhudza mpira.

 

Iweyo chikonzero chako ndichotani pa nkhani ya mpira?

Ndimafunitsitsa nditakasewera m’matimu akuluakulu a kunja monga ku Mangalande olo ku Spain.

 

Pomaliza tsogolo la mpira wa pa Malawi umaliona bwanji?

Tsogolo lilipo koma chofunika ndi chakuti akuluakulu komanso makampani ngakhalenso boma aziyikapo mtima. M’dziko munotu muli anyamata abwino kwambiri pankhani ya mpira koma chomwe chimavuta ndi chilimbikitso basi.

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.

Comments are closed.

« »