Chichewa

Ulangizi wa pafoni uthandiza alimi

Listen to this article

Ndizachidziwikile kuti dziko la Malawi limadalira ulimi pa chuma chake ndipo ambiri mwa alimi m’dziko muno ndi alimi a minda ing’onoing’ono omwe amadalira alangizi kuti awafikire ndi njira komanso luso la makono pa ulimi.
Nawonso akatswiri a za ulimi omwe akukangalika kuchita kafukufuku pofuna kupeza njira komanso luso la makono paulimi amadaliranso alangizi kuti afikire alimi ndi luso ndi njira za makonozi.
Koma ngakhale izi zili choncho, ntchito za ulangizi zikukumana ndi mavuto ochuluka monga mlili wa Edzi, kuchepa kwa zipangizo zogwiritsa ntchito, ufulu pankhani za misika komanso ufulu wa demokalase kungotchulapo ochepa. Kupatula zonsezi, onse okhuzidwa ndi ntchito za ulangizi akhala akutsatira njira za ulangizi zodalira kuti mlimi ndi mlangizi akumane maso ndi maso.
Pofuna kuchepetsa ena mwa mavutowa polingaliranso kuti chiwerengero cha alangizi chikuchepa, unduna wamalimidwe kudzera ku nthambi ya ulangizi mogwirizana ndi mabungwe omwe siaboma, adakonza msonkhano wokambirana zolimbikitsa ulangizi pogwiritsa ntchito luso lamakono pogwiritsa ntchito malo oimbira foni kapena kuunguza zinthu pa Internet.
Msonkhanowu udachitikira ku Malawi Institute of Management mumzinda wa Lilongwe ndipo udabweretsa pamodzi akatswiri kuchokera ku unduna wa zamalimidwe, sukulu za ukachenjede za Luanar komanso NRC ndi makampani komanso mabungwe a Self-Help Africa, TNM, Airtel, Farm Radio Trust, Technobrain, atolankhani, alimi komanso ena ambiri.
Zolinga za msonkhanowu zidali zitatu. Cholinga choyamba chidali kukhazikitsa masomphenya a kayendetsedwe ka malo olandira ndi kupereka mauthenga a ulangizi (call centre). Chachiwiri chidali kugawana nzeru pakayendetsedwe ka malowa.
Chomaliza chidali kupangana momwe dongosolo la malowa liyendere kuno ku Malawi.
Akatswiri osiyanasiyana adapereka maganizo awo pakayendetsedwe ka malo amenewa.
Call centre ndi malo omwe alimi amene ali ndi foni za m’manja amatha kuimba kapena kutumiza mauthenga kufuna kupeza ulangizi ndipo akatero amalandira mayankho malingana ndi zomwe adafunsa.
Yemwe adatsogolera kupereka maganizo ake adali mkulu wa kampani ya foni za m’manja ya Airtel. Atatha mkulu wa Airtel, padabwera anthu asanu ndi awiri omwe adaperekanso maganizo awo motsatizana.
Anthu adaloledwa kufunsa mafunso ndi kupereka ndemanga pa zomwe akuluakuluwa adalankhula.
Pamapeto pa zokambirana, anthu onse adagwirizana kuti njira yogwiritsa ntchito malowa yingathandize kwambiri kupereka ulangizi kwa alimi makamaka pano pomwe chiwerengero cha alimi chikuchuluka kuyerekeza ndi alangizi.
Pali chiyembekezo choti malowa athandiza kutukula nchito za ulimi popereka ulangizi woyenera panthawi yake.
Ndipo poyankhula pa mwambowu, mmodzi mwa akuluakulu mu unduna wa za malimidwe yemwenso adali mlendo wolemekezeka pa mwambowu Dr Wilfred Lipita adati iye akukhulupilira kuti umphawi ukupita mtsogolo pakati pa alimi kaamba kosowa uthenga wokwanira ndipo podzindikira kufunikira kogwiritsa ntchito njira zamakono pa ulangizi, unduna wake wakhazikitsa komiti yapadera yoonetsetsa kuti luso lamakono likugwiritsidwa ntchito bwino pa ulangizi yotchedwa the National Agricultural Content Committee for ICT.
“Ngati unduna, tikudzindikira kufunikira kogwiritsa ntchito luso lamakono pa ulangizi kotero takhazikitsa komiti yapadera yoonetsetsa kuti pasakhale chisawawa pogwiritsa ntchito luso lamakono pa ulangizi,”adatero Lipita.
Ngati muli ndi mafunso kapena ndemanga pa nkhaniyi, lemberani kalata kapena kuimba lamya kwa:
Head
Extension Department
P. O. Box 219
Lilongwe
01 277 260.

Related Articles

Back to top button