Chichewa

Ulimi wamthirira usangokhala nyimbo

Mkonzi,

Ndimamva chisoni njala ikamagwa m’dziko muno chifukwa choti mwagwa chilala pamene tili ndi nyanja ndi mitsinje yambiri yomwe simaphwera nthawi yachilimwe, zomwe zingatithandize paulimi wamthirira.

Mthirira ungatipulumutse
Mthirira ungatipulumutse

Kodi, Amalawi anzanga, ndi zoona tizifa ndi ludzu mwendo uli m’madzi? Ndithudi maiko a anzathu amene sadadalitsidwe ndi nyanja ndi mitsinje ngati ku Malawi kuno amaseka chikhakhali akationa tikupempha chakudya kumaiko ena chonsecho tili ndi kuthekera kopeza chakudya chokwanira chaka ndi chaka choti chikhoza kudyetsa fuko la Malawi chaka chathunthu popanda vuto lililonse.

Vuto ndi boma lathu lomwe limatsogoza ndale kuposa chitukuko cha dziko ndi miyoyo ya anthu ake. Ndi liti lija adayamba za kulimbikitsa ulimi wamthirira pofuna kuthetsa vuto la njala m’dziko muno? Tonse tikudziwa bwino za nkhambakamwa ya Green Belt Initiative. Ndani lero angandilozere kuti Green Belt ili apa? Tidamva zoti boma lagula mathirakitala kuchokera ku India kuti athe kuthandiza alimi m’midzimu pachitukuko cha ulimi. Ali kuti ndipo akuchita nawo chiyani pano?

Kugula chakudya kumaiko akunja pofuna kudyetsa fuko la Malawi kuli apo, ndi bwino koposa kuti boma likhazikitse mfundo zolimbikitsa ulimi wamthirira mmbali mwa nyanja ya Malawi ndi kuchigwa cha Shire komanso mmbali mwa mitsinje ina monga North ndi South Rukuru, Runyina, Limphasa kuchigawo cha kumpoto; mitsinje ya Linthipe, Lilongwe ndi Bua m’chigawo cha pakati; mitsinje ya Thutchira ndi Ruo kummwera mongotchurapo malo ochepa.

Related Articles

Back to top button