Nkhani

Ulova wafika posauzana 

Listen to this article

Adatenga digiri ya uphunzitsi mu 2010 ku Chancellor College (Chanco), kaamba kosowa ntchito, tsopano wachoka m’tauni ndipo akukhala kumudzi komwe akusaka timaganyu.

Chiyembekezo cha ntchito chidadza pa 23 July 2016 pamene bungwe la Global Warming Research International (GWRI) lidalengeza mwayi wa ntchito pokhoma mauthenga m’mitengo ku Dedza.

Osaka ntchito mazanamazana kuyesera mwayi wawo ku Golden Peacock mumzinda wa Lilongwe mmboyomu Wolemba
Osaka ntchito mazanamazana kuyesera mwayi wawo ku Golden Peacock mumzinda wa Lilongwe mmboyomu
Wolemba

Udali mwayi wa nzama kwa Joackim Nyanda pomwe bungweli limafuna amene ali ndi pepala la JCE ndipo amene ali ndi loposera apa akhala ndi mwayi waukulu kupeza ntchitoyo.

Ndi mtima wonse, Nyanda, wa zaka 30, adakhulupirira kuti mwayi wa ntchito aupeza chifukwa cha digiri yomwe akusunga. Akadadziwa akadaphika therere. Sudali mwayi koma tsoka chifukwa bungwelo lidamuyeretsa m’maso pomubera ndalama dzuwa likuswa mtengo.

Izi ndizo zikuchitika m’maboma a Dedza, Ntcheu, Mangochi komanso Kasungu komwe anthu akulira ndi bungwe la GWRI powanamiza kuti awapatsa mwayi wa ntchito, malinga ndi anthu komanso apolisi amene talankhula nawo.

“Kudakhomedwa uthenga m’mitengo kuti bungweli likufuna anthu oti awerengere chiwerengero cha anthu m’dziko muno. Amati tilembere kudzera pa E-mail kapena kutumiza uthenga pafoni.

“Udali mwayi wanga, ndidatumiza kudzera pafoni chifukwa E-mail imabwerera. Nditatumiza, adandiyankha kuti athokoza potumiza uthengawo ndipo adati nditumize K1 000 kumpamba pa 0882 453 891 yomwe idzagwiritsidwe ntchito pogulira chakudya tsiku lomwe adzatiitanelo,” adatero Nyanda, yemwe ali ndi mwana mmodzi ndipo akukhala ku Dedza.

Uthengawo, womwe Tamvani yauona, udati anthu amwayi adzaitanidwa kuti akakumane kuholo ya Umbwi Secondary School pa 25 ndi 26 July nthawi ya 9 koloko mmawa.

Uthengawo udatinso amene adzachite mphumi adzapatsidwa ntchito yochita kalembera amene achitike miyezi isanu m’maboma a Lilongwe, Karonga, Nkhotakota, Salima, Ntcheu ndi Dedza ndipo ntchitoyi idzagwiridwa m’zigawo.

Poyang’anira ulova womwe wachuluka m’dziko muno, anthu pafupifupi 100 akuti adakakumana kuholo ya Umbwi pa 25 July zomwe zidadabwitsa mphunzitsi wamkulu pasukuluyi.

Mphunzitsiyu, Alick Mnzanga, adati iye adangodabwa anthu akusonkhana pasukulupo.

“Choyamba nditaona uthengawo, ndidaimba nambala yomwe idali pauthengawo chifukwa chomwe akulembera zoti adzakumana kuno pamene adali asadadzatidziwitse.

“Adandiyankha kuti abwera koma sadabwere, kenaka tidangodabwa anthu akutulukira. Titaimbanso nambalayo simapezeka ndiye ndidawauza anthuwo kuti abwerere,” adatero mphunzitsiyu.

Apa mpamene Nyanda limodzi ndi anzake adadziwa kuti aberedwa. Loto lopeza mwayi wa ntchito kwa Nyanda lidasandukanso la chumba.

Si ku Dedza kokha komwe aona zoterezi, nakoso ku Ntcheu, Mangochi ndi Kasungu akuti ena awakwangwanula masanasana m’dzina lopeza mwayi wa ntchito.

Gift Bengo wa m’mudzi mwa Zakutchire kwa T/A Champiti ku Ntcheu nayenso adamubera m’njira yotereyi.
“Sindigwira ntchito koma ndili ndi pepala la Fomu 4. Nditaona uthengawo, ndidangoti mwayi wangawo.

“Adati tikakumane ku holo ya New Era, umo mudali mu June, ndipo tidakakumana anthu pafupifupi 200 komwe tidauzidwa ndi eni sukuluyo kuti sakudziwa chilichonse ndipo manambalawo samagwiranso,” adatero.

Naye mneneri wa polisi ya Mangochi, Rodrick Maida, akuti kumeneko zidachitika mwezi wathawu ndipo amauzidwa kuti akakumane kusekondale ya Mangochi.

Koma anthuwo amene adalipo pafupifupi 80 atakakumana kusukuluko, adabwezedwako kuti sakudziwa chilichonse cha nkhaniyo.

“Panopa apolisi tikufufuza za nkhaniyi, koma vuto ndi loti manambala awo sakupezekanso zomwe zikupangitsa kuti kafukufuku wathu avute,” adatero Maida.

Tamvani atayesera kuimba pa nambala ya 0991 743 325 yomwe bungweli limati anthu azitumizirako uthenga wofunsira ntchito, sidapezeke mpaka pamene timalemba nkhaniyi.

Nayo nambala yomwe amati azitumizirako K1 000 ku Mpamba simapezeka. Titafufuzanso pa Google ngati bungwe la Global Warming Research International lilipo, palibe zotsatira zomwe tidapezapo.

Kodi bungwe loona zofalitsa mauthenga la silingathandizepo kupeza amene wawachita chipongwe anthuwa?
Mneneri wa bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (Macra), Clara Mwafulirwa, adati woyenera kuyankhapo pankhaniyi ndi a TNM osati iwo.

“Ukamatsegula Mpamba, umayenera ukhale ndi chiphaso chako kusonyeza kuti uthenga wonse umayenera upereke. Tafunsani a TNM amene angayankhepo,” adatero.

Mneneri wa kampani ya TNM, Limbani Msapato, adati sakufuna kulankhulapo pankhaniyi. “Momwe mukufotokozeramo nzovuta kuti ndilankhulepo,” adatero iye. Koma Titamupempha kuti awalangiza zotani omwe amagwiritsa ntchito mafoni a TNM, iye adati: “Sindikufuna kulankhulapo, dikirani ndiimbanso.” Koma sadaimbe kufikira nthawi yosindikiza nkhaniyi.

Malinga ndi bungwe la kafukufuku wa ziwerengero m’dziko muno la National Statistical Office (NSO) za 2014, anthu 8 mwa 10 alionse m’dziko muno sali pantchito yolembedwa.

Nduna ya zachuma, Goodall Gondwe, polankhula nthawi yomwe Nyumba ya Malamulo imakumana, adati malinga ndi mavuto a zachuma, boma lizingolemba apolisi, asirikali ndi anamwino.

Posakhalitsapa, khamu la anthu lidasonkhana ku Golden Peacock mumzinda wa Lilongwe komwe ankafuna kulemba antchito owerengeka chabe koma zidadabwitsa pamene anthu miyandamiyanda adasonkhana m’mizere yaitali kufuna kuyesa nawo mwayi wa ntchitowo.

Related Articles

Back to top button