Nkhani

Uve wanyanya m’misika

  • Akugwiritsa madzi a m’zithamphwi
  • Tituluka mumsika muno—mabutchala

Kafukufuku yemwe Tamvani wachita sabata ino waonetsa kuti uve wanyanya m’misika yambiri m’dziko muno, maka ya m’makhonsolo a mizinda ya Blantyre ndi Lilongwe kaamba koti mulibe madzi a m’mipope.

Masamba ngati awa amafunika kutsuka  asanagulitsidwe
Masamba ngati awa amafunika kutsuka asanagulitsidwe

Chifukwa cha kusowa ukhondo mumsika waukulu mumzinda wa Blantyre, mabutchala aopseza kuti ngati khonsolo sichitapo kanthu atuluka mumsikawu chifukwa akhala zaka ziwiri tsopano popanda madzi aukhondo.

Iwo akuti pakalipano akugwiritsa ntchito madzi am’zithaphwi potsukira nyama ndi zipangizo zomwe amagwiritsa ntchito, pomwe ena akuti amachita kukagula madziwo kutali ndi malo a bizinesi yawo.

Izi zikhoza kuika miyoyo ya ogula ndi ogulitsa nyama pachiopsezo chifukwa nyama yosasamalika bwino ikhoza kukhala gwero la majeremusi omwe athanso kuononga miyoyo ya anthu odya nyamayo.

Koma mneneri wa khonsoloyi Anthony Kasunda wati khonsolo ya Blantyre sikudziwa kuti kumsikawu kudadulidwa madzi.

Kasunda: Tsatirani  malamulo
Kasunda: Tsatirani
malamulo

“Timakhala ndi anthu oyang’anira misika ndipo amenewo amalumikizana ndi khonsolo pa nkhani za mabilu a madzi ndi magetsi ndi zina zonse. Nkhani mukunenayi ndi yachilendo kwa ife,” adatero Kasunda.

Loweruka sabata yatha, mabutchalawa adauza Tamvani kuti akhala akudandaulira khonsoloyi nthawi yaitali kuti ikonze zinthu koma palibe chomwe chikuchitika kupatula kulonjeza.

Iwo adati mu 2014, khonsoloyi idakazula mamita a madzi ponena kuti mabilu akukwera kwambiri, koma akuti adasiya lonjezo loti nkhani yokhudza madzi aikonza.

“Butchala aliyense ali ndi chipinda chake chomwe amagulitsiramo nyama. Pomanga msikawu, chipinda chilichonse chidali ndi mpope wamadzi, koma mu 2014 khonsoloyi idadzazula mamita. Kuchokera apo mpaka lero tilibe madzi,” adatero butchala wina.

“Panopa tikugwiritsa ntchito madzi amene amangodzitulukira pansi pafupi ndi msikawu, pena timakagula m’zigubu.”

Iye adati poyamba akamalipira ndalama za lendi amaphatikizaponso za madzi malinga ndi bilu yomwe yatuluka ndipo khonsoloyi ndiyo inkakalipira ku Blantyre Water Board.

“Sitimvetsabe chifukwa chomwe adachotsera madziwa, chifukwa timalipira, koma tidadabwa akudzachotsa mamita Achikhala amadzachotsa ndi a Water Board bwezi mwina titadziwa chifukwa chake,” adatero.

Paganizo la mavendawa lotuluka kumsikawu, Kasunda adati malamulo oyendetsera mzinda wa Blantyre amaletsa kuchita malonda paliponse kotero ndi kuphwanya malamulo kutuluka mumsikawu.

“Aliyense wochita malonda mumzinda wa Blantyre akuyenera kutsatira malamulo onse ndipo palibe chifukwa choti wina aphwanye malamulowo mwadala,” adatero.

Kupatula nkhani ya madzi, mabutchala a mumsika wa Blantyre ati nkhani ina iwatulutse mumsikawu ndi anthu ena amene akugulitsa nyama mwachisawawa popanda zikalata.

“Kukumabwera galimoto zitanyamula nyama ndi masikelo awo. Akumagulitsa nyama paliponse pamene ife amatikaniza kutero. Chifukwa cha izi, nyama yathu sikuyenda malonda.

“Tadandaula koma sizikumveka. Anthuwa alibe zikalata zogulitsira nyama koma sakuletsedwa. Timadula chiphaso chophera nyama chomwe ndi K21 000, chipinda chogulitsira timalipira K17 000 pamwezi, koma ena akuwalola kumagulitsa nyama paliponse,” adatero mmodzi wolankhulira mabutchalawo.

Pankhaniyi, Kasunda adati khonsolo sidapereke chiphanso cha bizinesi kwa ogulitsa nyama paliponse “ndipo anthu amene amakhazikitsa bata mumzinda wathu [ma rangers] amalanda malonda alionse amene akuchitikira malo osayenera”.

Nawo msika wa ku Limbe mumzindawu mavutowa aliponso chifukwa nakonso madzi adawadulira mu 2014.

Podula madziwo, khonsoloyi idatsegula malo amodzi amene anthu onse mumsika akutungapo.

Ku Lilongwe, misika ya Tsoka, Kawale, Biwi ndi Mchesi ukhondo ulipo kaamba koti madzi aukhondo aliko.

Koma mumsika wa Lilongwe Central womwe ndi waukulu, uve akuti wafikapo pamene mavenda akugwiritsa ntchito madzi amumtsinje wa Lilongwe.

Kondwani Juwawo, yemwe amagulitsa tomato mumsikawu, adati akafuna madzi abwino ndiye amakagula kwa munthu wina pafupi ndi msikawo.

“Madziwa ndi odula chifukwa ndi a munthu osati a Water Board. Ngati tilibe ndalama timakatunga kumtsinjeko kudzatsukira tomato ndi kuwaza ndiwo zamasamba kuti zisanyale,” adatero Juwawo.

Ku Mzuzu zinthu akuti zili bwinoko chifukwa misika ya Luwinga, Zigwagwa ndi msika waukulu wa Mzuzu mulibe mavuto a madzi.

Lachitatu Tamvani itazungulira misikayi, yomwe imakhala ndi anthu ambiri, zinthu zidaoneka zosinthirako pamene wamalonda aliyense adali ndi mwayi wa madzi aukhondo m’misikayo.

Mkulu woona za umoyo mumzinda wa Mzuzu, Felix Namakhuwa, adati misika yonse kumeneko ili ndi madzi monga njira imodzi yolimbikitsa nkhani za ukhondo.  “Timawalimbikitsa za kufunika kotsuka malonda awo komanso kusamba m’manja asadayambe kugulitsa malonda awo. Ichi n’chifukwa chake venda aliyense ali ndi madzi m’misikayi,” adatero Namakhuwa.—Zowonjezera: Martha Chirambo ndi Steven Pembamoyo.

Related Articles

Back to top button