Chichewa

Vuto la madzi lakula ku Mulanje

Listen to this article

Anthu a m’dera la mfumu Mpweshe komanso Khunyeliwa m’dera la T/A Juma m’boma la Mulanje akuvutika kuti apeze madzi aukhondo chifukwa cha kuchepa kwa mijigo m’midzi mwawo.

Mudzi wa Mpweshe, womwe uli pamtunda wa pafupifupi makilomita 55 kuchokera pa boma, uli ndi mjigo umodzi okha pomwe mabanja oposa 400 amakatunga madzi.

Malinga ndi mfumu Mpweshe, kuchepa kwa mijigoko kukudzetsa mavuto osiyanasiyana chifukwa amayi ndi atsikana amakhala pamizere italiitali kuti apeze mpata wotunga madzi, komanso ambiri mwa iwo amayenda ulendo wautali kuti akafike komwe kuli mjigowo.

water-tap2

“Mjigo womwe uli m’mudzi mwathuwo adaukumbira kumbali kwenikweni kwa mudzi wathu komwe ndi kumalire ndi mudzi wa Khunyeliwa womwenso uli ndi mavuto a madzi, choncho kutunga madzi pamjigowo kumakhala kolimbirana kaamba ka kuchuluka kwa anthu,” idatero mfumuyo.

Malinga ndi mmodzi mwa ogwira ntchito muofesi yoona za madzi m’boma la Mulanje, Medson Bwezani, ndondomeko za madzi zimati mjigo umodzi umayenera kupereka madzi kwa anthu okwana 200, pomwe mpope umodzi umayenera kumagwiritsidwa ntchito ndi anthu 250.

Mjigo wina womwe mudziwo udali nawo utaonongeka m’chaka cha 2007 mudziwo sudalandirenso mjigo wina.

Mfumu Mpweshe idauza Mana kuti kwa zaka pafupifupi 8 mudziwo wakhala m’mavuto otere ngakhale kuti iwo ndi anthu a m’mudzi mwawo akhala akunena za vutolo kukhonsolo komanso kwa mabungwe omwe akugwira ntchito m’deralo kuti awathandize.

Poyankhulapo, mkulu woyendetsa zitukuko m’boma la Mulanje, Humphrey Gondwe, adati izi n’zomvetsa chisoni chifukwa kupereka madzi aukhondo kwa anthu ndi imodzi mwa ngodya za chitukuko cha dziko lino.

Gondwe adati vuto lomwe lilipo ndi lakuti pazitukuko zomwe atsogoleri a m’deralo adapereka chaka chino kukhonsolo kuti iwathandize, sadaikepo chitukuko cha madzi. Choncho n’kovuta kuti khonsolo iwapatse mjigo anthuwo msanga.

Chinthu china chomwe chikukulitsa vuto la madzilo n’chakuti m’mudzimo mulibe chitsime kapenanso mtsinje woti anthu angamakatungeko madzi ogwiritsa ntchito zina.

 

Related Articles

Back to top button
Translate »