Nkhani

Waganyu: Nzeru zayekha adaviyika Flames

Akulu adati nzeru zayekha adaviyika nsima m’madzi. Lero tikuti nzeru zayekha adaviyika Flames m’madzi. Zidachitika ku Algeria sindizo, timu yathu aivupulanso.

M’sabata imodzi Algeria yatipuntha 5-0. Izi zikusonyeza kuti pamasewero anayi amene Flames yasewera yachinyitsa zigoli 9.

Aganyu kudzanso akatswiri alankhulapo zoti Young Chimodzi achite koma zikuoneka kuti bwana Young sangamvenso zamunthu. Lero ndi izo tsopano, titani apa?

Kodi nchifukwa chiyani Robin Ngalande mukumuseweretsa kumbali pamene tili ndi osewera amene angachite bwino kuposa iye? Robin amasewera kutsogolo nthawi zonse koma inu mwamusintha.

Anthu akuti tayesani osewera monga Fisher Kondowe amene m’mbali amachita bwino. Chifukwa chiyani kuseweretsa Chiukepo Msowoya amene ku Mozambique sakusewera? Nanga mukusiiranji osewera ngati Deus Nkutu amene wachinya zigoli 15 muligi?

Bwana Chimodzi mukutithetsatu mawu inu. Bwanji osamvera zomwe anthu akulankhula kuti zikanike zokha?

Kumbukirani, chisankhidwireni kukhala mphunzitsi wa Flames tangopambana magemu atatu, Ethiopia, Benin ndi Chad ndipo talephera magemu 10. Kodi bwana Chimodzi zikuvuta pati?

Pano mwayi wochita bwino wacheperatu chifukwa tikuyenera tikaphe Ethiopia kwawo komanso kupha Mali pamene ikubwera kumudzi kuno zomwe zikukaikitsa. Mali ikukonza zodzapha Flames podziwiratu kuti gemu yawo ndi Algeria zikawavuta.

Related Articles

Back to top button