Nkhani

Waganyu: Tisaloze chala Mtawali

Listen to this article

Sabata yatha zidatigwera, Junior Flames kupunthidwa ndi Zambia 2-1. Tisabise, Zambia idasewera bwino. Mwayi ndi goloboyi wathu, apo biii! tidakasamba zenizeni.

Ganizo la Ernest Mtawali ndi lakuti akasinthe zinthu ku Zambia. Tingopemphera mwina chozizwa chikachitike koma kuona kwathu izi zikavutirapo.

Kukonzekera kwathu nkodandaulitsa. Mpikisano ngati umenewu koma tikungokhala ku Chiwembe pamapeto nkumati takonzeka kukapha Zambia.

Timaganiza tionetsa chidwi pa anyamatawa polingalira kuti imeneyi ndi timu yomwe tidyere mawali.

Timadandaula kuti sitichita bwino ku Afcon ndi timu yaikulu. Eya tikuyenera kudandaula chifukwa mpira wathu sitiyambira patali. Tili ndi osewera amene akumenya Flames yaikulu koma sadapondemo mu Under-17 kapena 20.

Lero tili ndi anawa koma thandizo palibe. Mphunzitsi wa Zambia, Hector Chilombo, adati dziko lawo likupereka thandizo kwambiri kutimu yake chifukwa akudziwa kuti tsogolo lonse lili mwa achisodzera.

Ndizodziwikiratu, pofika zaka zitatu zikudzazi Zambia idzakhala ikuchita bwino mukaona mmene akuchitira.

Vuto lathu sitithandiza achisodzerawa. Mwachitsanzo, timu ya Flames yaikulu idalonjezedwa K100 000 aliyense akapha Benin. Koma anawa posewera ndi Zambia osawalonjeza kanthu.

Flames yaikulu yakonzeredwa masewero ambiri opimana mphamvu koma anawa ayi. Mmalo mwake kumakumana ndi Azam Tigers kapena Mighty Wanderers.

Ndiye makochi a Flames yaikulu akamati akukonza timu amatanthauza chiyani pamene timu yaying’ono ikusiyidwa?

Related Articles

Back to top button
Translate »