Wamitala afera khunkha

July 14, 2013 • Nkhani • Written by :

‘Adali kuchipinda kwa chibwenzi’

Zidali ku Thyolo si ndizo. Mkulu wina yemwe akuti adali wamitala watisiya ali mkati mogawana chikondi ndi chibwenzi chamseri atazembera akazi akewo.

Malinga ndi mneneri wa polisi ya Thyolo, Edith Likaka, bamboyo, yemwe dzina lake ndi Distoni Liboti, wazaka 35, adali ndi akazi awiri omwe akukhala nyumba yakeyake koma m’mudzi umodzi. Mkuluyu akuti adalinso ndi chibwenzi chamseri, dzina lake Elizabeth Frank.

Usiku wa Loweruka pa 6 July, Liboti adanyamuka kwa mkazi wamkulu ponena kuti akagona kwa mkazi wamng’ono. Akuti adanyamukadi kwa mkazi wamkuluyo, yemwe adali naye ana atatu, koma sadakafike kwa mkazi wachiwiriyo, yemwe adalindo naye ana atatu.

“Mmalo mwake adakathera kwa chibwenzi chomwe chili ndi mwana mmodzi yemwe sadali wake wa Liboti. Awiriwo atacheza kanthawi, adakokerana kumphasa kuti akamasukirane,” adatero Likaka.

Akuti ntchito yakuchipinda ili mkati, Elizabeth, yemwe ali ndi zaka 32, adadabwa kuona Liboti wasiya kutakataka. Izi akuti zidamudabwitsa ndi kumuziziritsa.

“Elizabeth adatiuza kuti panthawiyo zidachitika modzidzimutsa chifukwa poyamba pa machezawo zonse akuti zidali bwino. Iye akuti adamukankhira kumbali mwamunayo ndi kuthamangira kwa abale ake kukawauza zomwe zachitikazo,” adatero Likaka.

Abale a mkazi akuti adapita kwa achibale a mwamuna kukanena za ngoziyo koma panthawiyo n’kuti akuganiza kuti mwamunayo wangokomoka.

Achibale a Liboti adakwiya ndi nkhaniyo ndipo maphokoso adayamba koma apolisi adabwera msanga kudzalanditsa.

“Chimavuta n’chakuti akuchimuna samadziwa kuti mbale wawoyo adali ndi mkazi wina kupatula akazi awiriwo. Izi zidawaganiziritsa achibalewo kuti mwina pachitika kanthu kuti mbale wawoyo amwalire mwadzidzidzi,” adatero Likaka.

Thupi  la malemulo akuti lidatengeredwa kuchipatala cha boma cha Thyolo komwe adakatsimikiza kuti Liboti wamwalira ndi nthenda ya kuthamanga magazi (high blood pressure).

Mneneri wa polisiyo akuti sadamange aliyense pankhaniyi chifukwa zomwe achipatala adapeza zikunena kuti malemuyo sadachitidwe chipongwe chilichonse ndi munthu.

Anthuwa akuchokera m’mudzi mwa Mwitere, kwa STA Nanseta m’bomalo.

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.

Comments are closed.

« »