Nkhani

Watsalawatsala Lachiwiri likudzali, Chisankho chachibwereza chayandikira

Listen to this article

Mitima ili dyokodyoko kufuna kudziwa kuti kodi ndani adzasenze udindo wotumikira anthu m’madera osiyanasiyana pachisankho chachibwereza chomwe chiliko Lachiwiri likudzali malingana ndi ndondomeko ya bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC).

Malingana ndi bungweli, pakutha kwa sabata yamawa, anthu akhala akudziwa yemwe adzakhale phungu wa kunyumba ya malamulo kudera la kumadzulo kwa boma la Mchinji komanso makhansala  m’mawodi a Bunda m’boma la Kasungu, Kaliyeka m’boma la Lilongwe, Bembeke m’boma la Dedza ndi Sadzi m’boma la Zomba.

Mphamvu yosankha atsogoleri yagona mwa anthu ngati awa
Mphamvu yosankha atsogoleri yagona mwa anthu ngati awa

Zisankho zachibwereza zimachitika ngati yemwe adali woimira dera wamwalira kapena pazifukwa zina watula pansi udindo ndipo munthu wina akuyenera kulowa mmalo mwake kuti apitirize ntchito yake.

Dyokodyokoyu waonekera pomwe Tamvani adazungulira m’zipani zonse zomwe zikupikisana nawo pazichisankhozi kumva maganizo awo ndipo zosangalatsa nzakuti chipani chilichonse chalumbira kudzatenga mipando yonse.

Woyendetsa zisankho m’chipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP) Kondwani Nankhumwa adati palibe chokaikitsa kuti oyimirira chipanichi adzapambana chifukwa zonse zikuoneka kumisonkhano ya kampeni.

“Kulikonse komwe tayenda kukachita msonkhano wakampeni talandira sapoti yaikulu kwambiri moti ena aiwale chifukwa oyimirira chipani cha DPP akudzatenga mipando yonse mosakaikitsa,” adatero Nankhumwa.

Naye woyendetsa zisankho m’chipani cha Malawi Congress Party (MCP) Maxwell Thyolera adati onse otsatira chipanichi akonzekere chisangalalo pakutha kwa tsiku Lachiwiri pa 1 November chifukwa oyimirira chipanichi akudzaonetsa mphamvu za chipani.

“Chipani cha MCP ndi chipani chachikulu kwambiri ndipo aliyense amadziwa zimenezi. Pano ndikuuzeni kuti dzuwa likamadzati thii kulowa Lachiwiri, kudzakhala chisangalalo chokhachokha kuchipani cha Congress,” adatero Thyolera.

Kumbali yake, wogwirizira mpando wa mtsogoleri wa chipani cha Peoples (PP) Uladi Mussa adati chilichonse chakonzedwa kale chomwe chatsala nkuti oyimirira chipanichi m’mipando yanenedwayi adzalandire nyota zawo.

Iye adati chokhumudwitsa n’chimodzi chokha chomwe ndi nthawi yopangira kampeni yomwe yaperekedwa ndi bungwe loyendetsa zisankho, koma ngakhale zili chomwechi, chipanichi chidzapambana mosavuta.

“Sitikuyang’ana mmbuyo koma mtsogolo basi. Ngakhale apereka nthawi yochepa ya kampeni [masiku 9 okha], ife tilibe nkhawa. Anthu amachidziwa kale ndi kuchikonda chipani cha PP kotero akungoyembekeza kudzatsimikizira izi pa 1 November,” adatero Mussa.

Mneneri wa chipani cha United Democratic Front (UDF) Ken Ndanga adati chipanichi chakhala chikukumana ndi akuluakulu a m’madera momwe muchitike chisankhochi kukambirana za momwe angayendetsere nkhani ya chisankhoyi.

“Atsogoleri onse a m’madera momwe mudzakhale zisankho atitsimikizira kuti muli odzayimirira chipani cha UDF amphamvu ndipo tikupanga kampeni yamphamvu yomwe tikukhulupirira kuti palibenso wina yemwe angapambane kuposa oyimirira UDF,” adatero Ndanga.

Iye adati pomwe padali vuto ndi dera lomwe kukupikisana ofuna mpando wa uphungu wa kumadzulo kwa boma la Mchinji komwe ntchito yofufuza odzayimirira chipanichi idali mkati pofika Lachiwiri lathali pomwe amalankhula ndi Tamvani.

Sabata ziwiri zapitazi, zipani za ndale zakhala zili kalikiriki kuyenda m’madera onse momwe muchitike zisankhozi kukopa anthu kuti adzaponyere voti oyimirira zipani zawo ndipo chosangalatsa n’chakuti pamisonkhano yonseyi sipadamvekeko zazipolowe.

Wachiwiri kwa mneneri wa bungwe la MEC Richard Mveriwa adati chosangalatsa n’chakuti chitsegulireni misonkhano yokopa anthuyi pa 20 October, zinthu zakhala zikuyenda bwino popanda zokokanakokana pakati pa zipani kapena zimpani ndi bungweli.

Iye adati anthu odzathandizira kuyendetsa chisankhochi adayamba maphunziro awo pa 27 October ndipo misonkhano ya kampeni idzatsekedwa mawa pa 30 October, kukonzekera kudzaponya voti pa 1 November.

“Kumbali yathu, chilichonse chili mmalo mwake moti ndife okonzeka kudzayendetsa chisankho chimenechi mosavuta. Chomwe tingapemphe Amalawi n’chakuti apitirize kusunga mwambo kuyambira pano mpaka chisankho chidzathe,” adatero Mveriwa.

Malingana ndi ndondomeko ya kayendetsedwe ka chisankhochi, zipangizo zoponyera voti zidzayamba kuperekedwa m’malo a mavoti pa 30 October tsiku lotseka kampeni. Pa 1 November 2016, ndi tsiku loponyera voti ndipo pa 2 mpaka pa 4 November adzakhala masiku owerenga mavoti ndi kuulutsa opambana pomwe pa 7 November mpomwe maina a opambana adzasindikizidwe.

Related Articles

Back to top button