Wautali, kukasankha Baba Nijo

August 11, 2013 • Nkhani • Written by :

Abale anzanga, kumafewetsa moyo ndi bwino. Mwezi umenewu ndakhala ndi kufewetsa osati masewera.

Ndinapeza chikofiya changa, komanso mkanjo ndiye dzuwa likangobindikira ndikamva mwazini, umakhala ulendo wa mtauni kukafutulu, inde kumasula namazani. Kumeneko timadya udyi, phala la mpunga limenelo, komanso zipatso zochokera kutali ku Saudi Arabia zimene timazitcha kuti tende. Munthu wopanda chipembedzo ali chabe.

Nditachoka m’tauni usiku umenewo, n’kupita malo aja ndimakonda pa Wenela, ndidapezerera nkhani ya Moya Pete ili mkamwamkamwa.

“Koma mkulu uyu alibe mnzake. Ameneyu ndiye ofunika kuvala ufumu wamasiye wa Mfumu Mose. Alibe chibwana,” adali kutero mkulu amene adali ndi Abiti Patuma.

“Zoona. Mwaiwala muja ankasowera miyezi yambirimbiri anyamata aja Ajibu ndi Mustafa asanagwirizane ngati asiyirane mpando wolamulira ojiya, oitanira ndi osolola pano pa Wenela?” adafunsa Abiti Patuma.

“Nkhani yake si imeneyo. Kodi sunamve kuti Moya Pete anena kuti iwo anyamula kale mikondo, zibonga komanso zishango kuti akathamangitse ma Taifa amene akufuna kulanda theka la mtsinje wa Songwe?” adatero mkulu uja.

Kwa ine zonsezo zidali zachilendo.

“Ukunena zimenezo? Siumamvera wailesi iwe. Siukumva kuti otsatira Adona Hilida aneneratu kuti amene akumemeza nkhondo ndi wamsala,” adatero Abiti Patuma.

“Aaaaargh! Inu! Pamenepo ndiye kuti Polisi Palibe ikunena kuti mtsinje wa Songwe si wathu? Zonse tinkaphunzira m’kalasi zija ndi zachabe? Kuyerekeza kusintha mapu athu sikukusiyana konse ndi kusintha makaka a mbendera muja idachitira Mfumu Mose,” adatero wa pamalopo.

“Akulu nkhani muzizitsata. Chofunikatu n’kukambirana. Simukuona momwe Male Chauvinist Pigs ikuchitira. Kukambirana basi,” adatero mkulu uja.

Pajatu Baba Nijo atiuziratu kuti chiwerengero cha ofuna kuwagwetsa chiyenera kuchepa. Onse osapola liombo asayerekeza kukhala ndi lingaliro logwetsa Baba. Nzeru zakuya, munthu wamkulu, mkango, mphambe, utawaleza….

Nkhani ili mkamwamkamwa, idafika basi ina yochokera ku Thekerani. Mudadzala ndi anthu ovala malaya a makaka akuda, ofiira ndi obiriwira.

Ndidaitanira pambali mmodzi mwa anthuwo.

“Akulu wakuti?” ndidafunsa.

“Abale, titofuna ku Blantyre paboma,” adayankha mkuluyo, lilime lake lidali lopyapyala.

“Kuno sitimati paboma, koma mtauni. Kuli chiyani?” ndidatero.

“Ndinu mlendo kodi?” adandifunsa.

Ndidati ayi.

“Zoti ku Lilongwe kukhaladye moto hamuziwa?” adaliponya funso.

Abale anzanga, zina kupweteketsa mutu.

“Ife titonka ku Lilongwe kukasankha Baba Nijo,” adatero mkuluyo.

Ndidamuuza kuti ndikhoza kuwaperekeza kuboma, ayi m’tauni, chifukwa maofesi a Male Chauvinist Pigs siali patali.

Titafika uko, tidapezanso khamu la ena, akuimba nyimbo zawo.

Ngwazi chingwe chosaduka lero

Chosaduka, nthawi zonse

Ali ku Lilongwe

Ali naye ankhoswe

Nyimbotu zamakedzana. Kulamula kwake nako kwa make dzana.

Zivute zitani

Ife sitidzaopa

Tili pambuyo pa Baba…

Adayamba kutiwerenga mmodzimmodzi usanapse ulendo wa ku Lilongwe.

“Tsono tisananyamuke, aliyense alandiriretu chitupa chokavotera. Ndingoimba foni ku Lilongwe, zitupa tizipeza bwanji,” adatero yemwe amaoneka ngati tchalamasi, atavala baji.

Adalankhula kwa kanthawi pafonipo.

“Akuluakulu, aliyense kwawo n’kwawo. Akuti palibe zitupa zathu chifukwa ena apita kale kuchokera kuno,” adalengeza, misozi ikutsikira m’masaya.

“Heyi mwati bwa? Abale, ife tinakongola thalansipoti yobwerera kuno timati mukatipatsa ku Lilongwe yobwererera. Ulukhu upose apa?” adafunsa mkulu wa ku Thekerani uja.

« »