Chichewa

Woganiziridwa kutsatsa mafupa a munthu agwidwa

Listen to this article

 

Bambo wa zaka 25, James Kanjira, ali m’chitolokosi pomuganizira kuti amachita bizinesi yogulitsa mafupa a munthu m’boma la Nkhotakota.

Mkuluyu akuti adamugwira akutsatsa mafupa omwe akuganiziridwa kuti ndi a alubino.

Apolisi m’boma la Nkhotakota atsimikiza kuti adamanga Kanjira Lachitatu pa 27 April, 2016 pomuganizira mlanduwo pamene akuti amayembekezera kulandira ndalama za malondawo kuchokera kwa kasitomala wake, Stanley Kambewa, yemwe adali atawatsina khutu.

“Tamangadi James Kanjira yemwe amatsatsa mafupa a munthu. Iye adati mafupawo adali ku Kasungu. Polingalira zomwe zidachitika m’bomali sabata yatha kuti alubino adaphedwa, woganiziridwayu tamutumiza ku Kasungu kuti akamufufuze bwinobwino,” adatero mneneri wa polisi m’boma la Nkhotakota, Williams Kaponda.

Woganiziridwayo: Kanjira
Woganiziridwayo: Kanjira

Apolisi m’boma la Kasungu atsimikiza za kumangidwa kwa Kanjira ndipo ati mkuluyu adali mmodzi mwa anthu omwe amafunidwa ndi apolisi poganiziridwa kuti akukhudzidwa ndi kusowa komanso kuphedwa kwa alubino wa zaka ziwiri m’bomali.

“Tidatumiza uthenga m’maofesi onse a polisi a maina a anthu omwe tikufuna ndipo atabwera naye Lachitatu, lapitali tidamupana mpaka adaulula komwe kudali anzake ndipo tidawagwiranso komanso adalondola komwe adakwirira mafupawo,” adatero wachiwiri kwa mneneri wa polisi ku Kasungu Harry Namwaza.

Kanjira, yemwe amachokera ku Kasungu, akuti adapita ku Nkhotakota komwe adakumana ndi Kambewa n’kumutsatsa malonda a mafupa a munthu ndipo atagwirizana, wotsatsidwayo adakauza apolisi za nkhaniyo.

Kaponda adati Kanjira ataona kuti malonda atheka, adamasuka nkuulula kuti mafupawo adali a alubino ndipo adali ndi mnzake yemwe panthawiyo adali ku Kasungu.

Iye adati wotsatsidwayo atamva zimenezo nthumanzi idamugwira polingalira kuti sabata yatha nkhani ya alubino wophedwa m’boma la Kasungu idatchuka ndipo apolisi ali kalikiriki kusakasaka omwe adachita chiwembucho.

“Munthu ameneyu adachita bwino kwambiri chifukwa popanda anthu ngati iyeyo, ife sitingadziwe kalikonse ndipo tikufuna anthu ambiri ngati awa atamatithandiza choncho,” adatero Kaponda.

Iye adati mlanduwu padakalipano ndi wa mchitidwe omwe ukhoza kuyambitsa chisokonezo, womwe chilango chake chachikulu ndi miyezi itatu m’ndende potengera malamulo a dziko lino.

Koma Kaponda adati mlanduwu ukhoza kusintha chifukwa akumuganizira kuti adachita kufukula munthu wakufa, womwenso  ndi

mlandu paokha, koma zikadzapezeka kuti adachita kupha munthuyo, mlandu udzakhala wakupha, womwe atapezeka wolakwa akhoza kukaseweza kundende moyo wake wonse.

Nkhaniyo ili mkamwamkamwa, bungwe la Amnesty Internationa ladzudzula dziko la Malawi chifukwa cholephera kupereka chitetezo chokwanira kwa maalubino.

“Mwachitsanzo, mwana angabedwe bwanji m’nyumba usiku apolisi n’kulephera kufufuza mpaka mwana kuphedwa? Ndi moyo wa munthu tikukamba apawu, osati chomera ayi, ndiye pamayenera kuchitika zakupsa,” chatero chikalata cha chidzudzulo chomwe bungweli latulutsa.

M’chikalatacho, zadziwika kuti kuyambira mu 2014, anthu 12 achialubino aphedwa ndipo anthu asanu ndiwo akusowabe mpaka pano. Anthu 45 ndiwo adamangidwa pamilandu yokhudzana ndi kuphedwa kapena kusowa kwa anthuwa.

Koma nduna ya zachitetezo, Jappie Mhango, wati dziko la Malawi likuyesetsa kuchita zoti anthu amtunduwu komanso anthu omwe amaoneka ngati alibe mawu azitetezedwa mokwanira.

“Tili pakalikiriki ndipo sitilekera pomwepa, ayi, mpaka onse ochita izi tithane nawo. Nafe sitingakondwe kuti anthu azizunzika. Malamulo a dziko lino amati munthu aliyense ali ndi ufulu wokhala ndi moyo,” adatero Mhango. n

Related Articles

Back to top button