Nkhani

Wopanda chiphaso cha nzika sadzavota—MEC

Listen to this article

Bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) latsimikiza kuti chiphaso chakale chovotera sichidzanunkha kanthu pachisankho cha 2019.

Wapampando wa komiti yoona zophunzitsa anthu ndi kumwaza mauthenga a kavotedwe Commissioner Moffat Banda wati mmalo mwake bungwelo ligwiritsa ntchito zitupa za unzika.

Iye wati iyi ndi njira yokhayo yomwe bungweli lingathanirane ndi zachinyengo zomwe zimapezeka panthawi yachisankho ndipo ndiyokomera anthu ndi zipani zonse.

“Njira yogwiritsa ntchito zitupa za unzika idzatithandiza kupewa anthu osafika zaka 18 kuti asadzaponye nawo voti komanso idzaonetsetsa kuti ndi Amalawi okhaokhadi omwe adzaponye voti,” watero Banda.

Iye wati apa, mpofunika kuti Mmalawi aliyense akalembetseretu ndi bungwe lolemba za unzika kuti asadzavutike panthawi yoponya voti kaamba koti zitupa zina zonse sizidzagwira ntchito.

Koma mkulu wa bungwe loyang’anira zamomwe zisankho zimayendera la Malawi Electoral Support Network (Mesn) Steve Duwa wati bungwe la MEC likhoza kudzikola lokha ngati siliyendetsa bwino za nkhaniyi.

Duwa wati kugwiritsa ntchito ziphaso za unzika, ndi njira yothandiza kuchepetsa zachinyengo koma potengera malamulo oyendetsera zisankho, Amalawi akadali ndi ufulu ogwiritsa ntchito zitupa zosiyanasiyana.

Malingana ndi lamuloli, munthu yemwe ndi Mmalawi ndipo adafika pamsinkhu woponya voti, akhoza kugwiritsa ntchito zitupa monga choyendetsera galimoto, choyendera m’maiko ngakhalenso kalata yochokera kwa amfumu, mbale wodalirika kapena kuntchito.

“Pokhapokha akumane nkusintha lamuloli msanga chifukwa malamulo omwe ife timadziwa amalola anthu kugwiritsa ntchito umboni uliwonse kuti ndi Amalawi choncho mposavuta ena ozindikira kudzatengera MEC kukhoti,” adatero Duwa.

Iye wati pakali pano bungwe la MEC likhoza kumalengeza zomwe lakonza popanda anthu kulankhulapo koma pamakhala ena akudikira kuti zinthu zikamadzapsa mpomwe adzayambe kusokosa.

“MEC izikonzeratu mokhota monse chifukwa sizingadzakhale bwino kuti nthawi yothaitha adzayambe kulimbana ndi anthu m’makhoti pankhani yophweka ngati iyi,” watero Duwa.

Zipani zina za ndale zati zilibe mangawa ndi bungwe la MEC chachikulu bungwelo lidzaonetsetse kuti munthu aliyense woyenera kuvota ndipo waonetsa khumbo, adzalandire mpata.

“Zanjirazo ife tilibe nazo ntchito koma tikungofuna kuti bungwe la MEC lidzapereke mpata kwa Amalawi ogwiritsa ntchito ufulu wawo oponya voti. Pasadzapezeke kuti nkhani yachitupa yalepheretsa munthu kuponya voti,” watero Mlembi wa Malawi Congress Party (MCP) Eisenhower Mkaka.

Mneneri wa chipani cha Peoples Party (PP) Noah Chimpeni adagwirizana ndi Mkaka kuti chofunika n’choti Amalawi asadzaphwanyiridwe ufulu wawo oponya voti.

“Nthawi ilipo, ngati akufunitsitsa kudzagwiritsa ntchito njira imeneyo, ndiye kuti awonetsetse kuti Amalawi onse apatsidwa mpata wolembetsa m’kaundula wa unzika,” adatero Chimpeni.

Wapampando wa bungwe la MEC Jane Ansah adati bungwelo lakonza ndondomeko yoti munthu aliyense sadzamanidwa mpata malingana ngati watsatira malangizo.

“Tikudziwa kuti si Amalawi onse omwe angakhale atalembetsa pofika tsiku loponya voti komanso ena akhoza kukhala kuti adalembetsa koma zitupa zawo sizidatuluke onsewo tawaganizira.

“Tapanga njira ziwiri, yoyamba, omwe alembetsa koma chiphaso sichidatuluke adzabwere ndi tiketi yolembetsera imene idzatithandize kuwazindikira mkaundula, yachiwiri, pochita kalembera wathu tidzakhala ndi ogwira ntchito ku bungwe la kalembera wa unzika omwe azidzathandizira,” adatero Ansah.

Related Articles

Back to top button