Wopha Wame akasewenza moyo wake wonse

Bwalo la milandu lalikulu m’boma la Salima Lachitatu lidagamula Limbani Maliro, mnyamata yemwe adapha Mlaliki Shadreck Wame kukasewenza moyo wake wonse.

Bwalolo lomwe lidalowa nthawi itangodutsa 6 koloko ya madzulo lidapereka chigamulochi m’nthawi yosakwana ola limodzi.

Adachita chobaya: Wame

Apa n’kuti Maliro ali zyoli pomwe makutu a anthu a nkhaninkhani omwe adafika kubwaloli kukamvera mlanduwu adali tcheru. Bwaloli lidadzadza moti ena mwa anthuwo adaima panja kutsatira zochitikazo kudzera m’mazenera.

Naye woweruza Esmie Chombo sadachedwe ndi zambiri koma kungolunjika mpaka kupereka chigamulocho chomwe chidaliza mayi ake a Maliro.

Ndipo khope yake ili chigwere, Maliro yemwe adalibe omuimira pamlandu adapempha Chombo kuti amumvere chisoni chifukwa ndi wachichepere, ali

ndi banja komanso amathandiza abale.

Koma popereka chigamulo chake, Chombo adati Maliro akuyenera kusewenza moyo wake wonse chifukwa mlandu womwe adapalamula ngwaukulu wosayenera munthu wachichepere.

Iye adatinso naye Wame adali ndi abale omwe amawathandiza moti ana ambiri omwe amawalipirira fizi pano apita m’sukulu zosakhala bwino chifukwa akulephera kukwanitsa kupeza fizi.

Malinga ndi mneneri wa polisi m’boma la Salima, Gift Chitowe, Maliro adauza bwalo la milandulo kuti adapha Wame poganizira kuti amasunga ndalama zambiri m’nyumba mwake.

“Atadya mutu poona katundu yemwe Wame amabweretsa pakhomopo, Maliro adaganiza zomupha kuti amubere bwino. Patsiku lomwe adamuphalo Maliro adagwidwa ndi matumba a chimanga omwe adanyamula pa wilibala usiku.

Koma mwatsoka adawathawa anthuwa pomwe ankagogoda pa nyumba ya a Wame kuti afufuze ngati adampatsadi chimangachi,” adalongosola Chitowe.

Iye adati Maliro adapepesa pa zomwe adachita ndipo amaoneka wokhudzika m’nthawi yonse ya mlanduwu.

Wame adaphedwa mwezi wa October, chaka cha 2016 ndipo Maliro dagwidwa patadutsa mwezi, m’boma la Thyolo.

Lolemba lapitali iyeyu adavomera kuti adaphadi Wame.

Share This Post