Chichewa

Yamikani ‘Headmaster’ Fodya wa Bullets

Listen to this article

Dzina la Yamikani Fodya lawanda. Uyutu ndi mnyamata wokankha chikopa kutimu ya Flames komanso ku Big Bullets. Iyeyu wapatsidwa maina osiyanasiyana kaamba ka luso lake lomwe ochemerera mpira akuliyamikira monga mwa dzina lake. BOBBY KABANGO akumva za mbiri yake.

Fodya: Mulungu akakonza palibe angatsutse
Fodya: Mulungu akakonza palibe angatsutse

Tikambire za mbiri yako…

Ndimachokera ku Balaka. Ndine wa nambala 7 kubadwa m’banja la ana 8. Ndinenso wokwatira ndipo ndili ndi mwana mmodzi dzina lake Favour.

 

Ku Bullets udabwerako liti?

Ndidafika mumzinda wa Blantyre mu 2009. Nthawiyo n’kuti kutangoyambika chikho cha Presidential Cup ndiye anthu adaona luso langa mpaka kundiitanira kutimuyi.

 

Udalandiridwa bwanji?

Kundirandira kudali bwino koma kupeza mwayi wosewera padavuta. Ndidapeza osewera ambiri, ngakhale ku training sindimapeza mwayi. Ngakhale kutulutsa timu yonseyo, mwayi wolowabe sumapezeka.

 

Nanga umasewera malo ati?

Nthawiyo ndimasewera pakati, malo amene ndimasewera ku Young Soccer ya ku Dedza.

 

Zidatani kuti uyambe kusewera kumbuyo?

Idangokhala pulani ya Mulungu chifukwa kochi wa timuyi panthawiyo, Meke Mwase, adandifunsa za malo amene ndimasewera ndiye ndidangoti kumbuyo. Basitu kuyamba kusewera kudali komweko.

 

Zidayamba kukuyendera m’chaka chanji?

Mu 2010. Chaka chimenechi ndidasankhidwanso wosewera amene wachita bwino kumbuyo. Koma kuchoka nthawiyo mpaka 2013 ndiye zidavuta chifukwa ndidavulala msana.

 

Wafala paliponse ndi luso lako, kodi ndi mankhwala?

Mbale wanga, Mulungu akakonza palibe amene angatsutse. Pamene sizimayenda ndimalimbikirabe kuti tsiku lina zidzayende. Palibe mankhwala koma mphamvu yake basi. Si nzeru zanga koma chifundo chake cha Mulungu.

 

Malo amene ukusewera ku Flames umalimbirana ndi Francis Mlimbika, kodi simuchitirana nsanje?

Francis ndi mbale wanga, ndimamupatsa ulemu ndipo ndimakondwera naye. Dziwani kuti nayenso Mulungu adamupatsa luso. Ngati lusolo lili la Mulungu, ine ndani kuti ndimuchitire nsanje?

 

Kodi ukungotchula za Mulungu bwanji? Uli mpingo wanji?

Mbale wanga, palibe munthu amene sadziwa kuti kumwamba kuli Mulungu. Ngakhale wakuba amadziwa. Tili m’masiku omaliza, palibe chomwe tingachite ngati iye palibe. Malembo amati ngati Iye samanga nyumba omangayo amanga pachabe. N’chifukwanso ndimatsogoza Mulungu pazonse. Ndikupemphera mpingo wa Seventh Day Adventist.

 

Ukutchulidwa maina osiyanasiyana, kodi mainawa adabwera bwanji?

Tili ku Cosafa, onenerera mpira amanditchula kuti Soul Brother ati chifukwa cha tsitsi langali limafanana ndi oimba a gulu la Soul Brothers kumeneko. Kunoko anthu andipatsa dzina loti Headmaster chifukwa ndimapisira malaya 90 minitsi.

 

Kodi sumeta chifukwa chiyani? Nanga kupisiraku?

Ndimasangalala ndi osewera mpira akale amene samameta wamba, mametedwe alerowa kudalibe. Komanso amapisira ngakhale ma jersey ndi makabudula awo adali aang’ono. Zimenezi zimandisangalatsa. Komanso ndimamukumbukira Chisomo Kamulanje amene adandiuza zambiri za malo amene ndimasewera aja. Pamene amachoka ku Bullets ndidanena kuti ndikufuna ndidzapange chinthu chomwe ndidzamukumbukire nacho.

Related Articles

Back to top button