Nkhani

Za pasipoti ya Gaba sizikumveka

Sabatayi yakhala yomvetsa mutu ndi nkhani ya Gabadihno Mhango.

Zachitika m’sabatayi aganyu zatiwawa ndipo tikufuna bungwe la FAM komanso timu ya Big Bullets afotokoze bwino za zaka za Gaba.

Sitikumvetsa zomwe lero FAM ikunena. Kuyambira chaka chatha mpaka lero zakhala zikumveka kuti matimu akunja agwa m’chikondi ndi Gaba. Aliyense amadziwa kuti zikapsa Gaba anyamuka m’dziko muno. Tsono panthawiyi Fam idali kuti?

Mwina Bullets imadziwa malamulo ake komabe monga FAM ndi manthu wa mpira m’dziko muno timaganiza kuti amulangiza Gaba kuti adikire kaye polingalira zaka zake. Nanga FAM siimatero bwanji?

Lero zonse zatheka, Gaba wapeza potentha ndiye mukubwera ndi malamulo? Bwanji osathandizana monga tonse Amalawi? Apatu zachitika ngati Gaba si wa m’dziko muno, chifukwa akadakhala m’Malawi bwezi titamuthandiza pamene matimu akunja akhala akukhetsa dovu ndi iye.

Gaba wakhala akusewera Flames, kodi panthawiyi FAM imavomereza bwanji kuseweretsa mwana wa zaka 16? Kodi timu ya Celtic yomwe yamulemba Gaba siimadziwanso zaka zake?

Nanga zidakhala bwanji kuti mpakapasipoti yake ipindidwe? Takhala tikumva Gaba akulankhula yekha kuti ali ndi zaka 20.

Izitu zikusonyeza kuti alipo wina amamuuza kuti adzibisa zaka za m’pasipotimo. Tsono ngati vuto lili pasipoti, bwanji amene adamuuza kuti apinde zaka apeze njira yokonzera vutoli?

Gaba adziwe kuti mwamuna sachepa, wafikapa akudziwa chabwino ndi choipa kotero sakuyenera kulola chilichonse. Zotere zitha kusokoneza tsogolo lake.

Related Articles

One Comment

  1. ndimadabwa kuti tonse tasanduka vitsilu tikuwona ndithu kuti ku Fam kulivuto koma tìkumangowasiya kuti agaluwa azisokoneza dziko pa nkhani yampira,kodi ndi xul yanji anapita iwo bwanji mwanayo akhala akumuseweletsa akudziwa kuti ndiwochepa bwanji sankamulangiza akubwela ku national team? mbuzi za Fam basi.

Back to top button