Nkhani

Zakudya za ziweto zasowa

Listen to this article

Mboma la Nsanje, ziweto monga ng’ombe, nkhosa ndi mbuzi zili pamoto chifukwa cha kusowa kwa chakudya.

Kwauma, ndipo tchire anthu atentha. Nthawi ngati imeneyi zaka zonse, ziweto akuti zimadalira kumtsinje wa Ruo komwe zimakadya bango, nsenjere ndi udzu wauwisi.cow

Koma chaka chino chifukwa cha madzi osefukira, Ruo wabweretsa mchenga wambiri zomwe zachititsa kuti bango ndi udzu wauwisi ukwiririke. Mulibemo msipu ulionse.

Malinga ndi gulupu Manyowa, ziwetozi zikudalira makoko a chimanga, nthochi kapena zikonyo mwinanso mango.

“Ziweto zambiri zikumasonkhana pansi pa mitengo ya mango kuti anthu akamathyola zidyeko. Chifukwa cha kusowa chakudya, ziweto zambiri zaonda,” adatero Manyowa.

Koma alangizi amalangiza kuti zikatere alimi amayenera kuti azikhaliratu atapanga zakudya za ng’ombe ndi mbuzi kuti azizipatsa nthawi ngati ino.

Manyowa akuti m’mudzi mwake palibe munthu amene adapanga zakudyazo chifukwa cha mavuto a madzi amene adakumana nawo.

“Palibe amene adapanga zakudya za ziweto. Kodi mmene zidalili kuno ungamupeze munthu akupanga zakudya za ziweto? Mlimi aliyense adali ndi chiyembekezo kuti ziweto zizikadyera kumadzi monga zikhalira nthawi zonse osadziwa kuti kukhala mchenga wotere,” adaonjeza.

Mneneri mu unduna wa zamalimidwe, Hamilton Chimala, akuti alimi akuyenera kumakhala okonzeka ngati akufuna ziweto zawo zipulumuke nyengo ngati ino.

“Maiko ena ngakhalenso kwathu kuno timalangiza kuti alimi akuyenera kumakonza chakudya cha ziweto nthawi yotere isadafike. Zimanezi zimathandiza nthawi ngati ino. Yankho pa vutoli ndi lakuti alimi ayambe kupanga zakudya kuti ziweto zisakhale pamavuto,” adatero Chimala.n

Related Articles

Back to top button
Translate »