Chichewa

Zig Zero: Mnyamata wa nyimbo za dansi

Listen to this article

Kuyambira kuubwana wake chimene amaganiza, kulota ndi kuchita ndi kuimba nyimbo basi. Inde, Mulungu adamudalitsa ndi liwu lanthetemya mnyamata ameneyu ndipo pano akugwiritsa ntchito luntha lomwelo kuti apeze chakudya cha tsiku ndi tsiku komanso zosowa pamoyo wake. Uyu ndi Joseph Alufandika, mnyamata wosangalatsa anthu ndi mingoli yokoma. CHIMWEMWE SEFASI adapezana naye poduka mphepo ndipo adacheza naye motere:

Kudyera pakamwa: Alufandika
Kudyera pakamwa: Alufandika

Ndikudziwe…

Dzina langa ndine Joseph Alufandika, ndipo ndine wosakwatira, ndimachokera kuchigawo chakumwera konkuno m’boma la Nsanje. Anthu okonda nyimbo za dansi amandidziwa ndi dzina loti Zig Zero.

 

Kodi kuimba nyimbo za dansi udayamba liti?

Kuimba ndidayamba pakale ndithu. Ndili kusekondale ndi pamene ndidazindikira kuti ndili ndi luso losangalatsa anthu kudzera mumaimbidwe, munyimbo za dansi.

 

Kodi kupatula kuimba umachitanso chiyani?

Inetu ndimapanga bizinesi komanso ndikupitiriza maphunziro kusukulu ya Malawi College of Accountancy komwe ndikuphunzira zoonkhetsa chuma.

 

Kodi chimbale chako chatsopano chituluka liti? Mutu wake ndi chiyani?

Chimbale changa chikuyembezereka kutuka kumapeto a mwezi wa August, chomwe chikhale ndi nyimbo 14 zomwe zaimbidwa m’Chichewa ndi m’Chingerezi. Ndipo kuyambira pa 3 August mpomwe nditawadziwitse Amalawi zambiri.

 

Kodi ndi mavuto ati omwe oimba nyimbo za dansinu mumakumana nawo?

Mavuto omwe timakumana nawo ndi monga kupita kuzoimbaimba koma osapatsidwa ndalama yomwe tinagwiriza. Kumeneku ife timaona ngati tikuponderezedwa komanso anthu ena kuti atukule luso lathu amafuna kuti tiwapatse ndalama.

 

Kodi nyimbo za dansi ngati zomwe umaimba iweyo ukuona kuti zikupita patsogolo?

Kunena mosanama, Chimwemwe uli apa, nyimbo zaimbidwa ndi achinyamata zikupita patsogolo kwambiri chifukwa anthu akati ali pamalo achisangalalo monga kuukwati, zinkhoswe, malo osiyanasiyana, chisangalalo chawo chimakhala chopambana chifukwa cha uthenga womwe tikumapereka kudzera m’nyimbo zomwe tikumawapatsira .

 

Kodi ndi anthu ati omwe unaimbapo nawo nyimbo limodzi chiyambireni kuimba pa Malawi pano?

Inetu chiyambireni kuyimba pa Malawi pano ndaimbapo nyimbo ndi anthu ambiri monga Marcus Pasanje wa Dare Devils, Blasto, BFB ndi ena ambiri.

 

Pomaliza tandiuze zomwe umakonda.

Ine ndimakonda kuimba ndi kumvera nyimbo. Nthawi zina ndimakonda kuyenda ndi kumaona malo osiyanasiyana ndi kukumana ndi anthu osiyanasiyananso.

Related Articles

Back to top button