Nkhani

Zionetsero zilipo la chiwiri pa 13 January

ave
Wamenyetsa nkhwangwa pamwala: Mtambo

Zafika pa payerepayere. Mabungwe 20 omwe si aboma amenyetsa nkhwangwa pamwala ponena kuti zivute zitani palibe chomwe chingalepheretse zionetsero za dziko lonse zomwe akonza kudzachita Lachiwiri likebwerali ati pofuna kuonetsa mkwiyo ndi mmene zinthu zikuyendera m’dziko muno.

Imodzi mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zakwiyitsa mabungwewa ndi ndalama zomwe bungwe loyendetsa ntchito zolimbana ndi matenda a Edzi la National Aids Commission (NAC) lidapereka kumagulu omwe sakhudzidwa pankhondo yolimbana ndi matendawa.

Mneneri wa mabungwe omwe akukonza zionetserozi, Timothy Mtambo, yemwe ndi mkulu wa bungwe la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), adati cholinga cha zionetserozi n’kudzudzula boma ndi mmene likuyendetsera zinthu zomwe adati zikupweteketsa Amalawi.

Mwa zina, mabungwe omwe si abomawa akuti sakukhutira ndi momwe chuma cha boma chikuyendera, kuchepa kwa chitetezo ndi kusalemekeza ufulu wa Amalawi.

Iwo atinso boma likuwonetsa kuphangira mphamvu posalemekeza nthambi zina za boma monga nthambi ya zamalamulo, zomwe zidayambitsa sitalaka ya nthambiyi ndipo anthu ambiri akuzunzika m’ndende kudikira milandu yawo.

Mabungwewa akudzudzula nkhani ya ndalama zokwana K5 miliyoni zomwe bungwe la NAC lidapereka kubungwe la mayi wa fuko Gertrude Mutharika la Beautify Malawi (Beam) ndi zomwe lidaperekanso ku gulu la Muhlakho wa Alhomwe.

Koma pomwe mabungwewa akukonza izi, mabungwe ena omwenso si aboma monga bungwe la achinyamata la Youth Empowerment and Civic Education (Yece) ati iwo sadzatenga nawo mbali paziwonetserozi.

Mkulu wa bungweli, Lucky Mbewe, wati omwe akukonza zionetserozi sadatsate njira yoyenera posafunsa maganizo a mabungwe ena.

“Zinthu ngati izi zimafunika kukambirana osati kungobwera ndi maganizo omangamanga kuti tichita zakuti ayi. Zimenezi n’zomwe zatipangitsa ife kuti tisatenge nawo mbali,” adatero Mbewe.

Koma Mtambo akuti mabungwe omwe akupatuka akugwiritsidwa ntchito ndi boma kuti asokoneze zionetserozo.

Mavenda a ku Lilongwe nawo ati sakugwirizana ndi ganizo lodzachita zionetsero polingalira zomwe zidaoneka pazionetsero zamtunduwu zomwe zidachitika pa 20 July 2011.

“Zomwe zidachitika pa 20 July 2011 zimatipatsabe mantha moti apa sitikufuna kutenga nawo mbali. Vuto lina ndi lakuti zikakhala chonchi malonda athu amasokonekera ndiye ife ayi,” adatero James Yelayela Soko, venda wakalekale, yemwe adatsogolerapo mavenda a mumzinda wa Lilongwe.

Atafunsidwa ngati akudziwapo kanthu pa zionetsero zimene zikukonzedwazi, mneneri wa likulu la polisi Rhoda Manjolo adati apolisi sadalandire pempho lililonse la munthu kapena gulu lofuna kupanga zionetsero.

Mneneri wa Khonsolo ya Lilongwe Tamala Chafunya Lachiwiri lapitali adati ofesiyi sidalandire kalata iliyonse yopempha kuti anthu adzachite zionetsero.

Poikapo maganizo ake, katswiri wa zandale Blessings Chinsinga adati zionetserozo si zolakwika chifukwa ndi njira imodzi yodzudzulira pomwe boma likulephera.

Iye adati mabungwe omwe si aboma ndi ntchito yawo kuonetsetsa kuti boma silikuphotchola pakagwiridwe kake ka ntchito ndiye ngati zinthu zikupotoka iwo akuyenera kupeza njira yowongolera.

Iye adati njira yabwino yowongolera mokhota n’kukambirana koma ngati njirayi yakanika mabungwe ayenera kupeza njira zina monga kukonza zionetserozo.

Mkulu wa bungwe loyang’anira mabungwe onse omwe si aboma la Congoma, MacBain Mkandawire, adakana kunenapo ngati bungwe la Congoma likugwirizana kapena kutsutsana ndi ziwonetserozi.

Iye adati bungweli lili mkati mwa zokambirana ndi mabungwe omwe akukonza ziwonetserowo kuti aunike ngati n’kofunika kutero kapena ayi.

Mafumu nawo aperekapo maganizo osiyanasiyana pankhaniyi.

Mfumu Liwonde ya ku Machinga idati kuchita zionetsero n’kutaya nthawi chabe chifukwa palibe phindu lomwe limaoneka.

Koma Inkosi Chindi ya ku Mzimba idati ngati anthu akuona kuti penapake sipadayende bwino ali ndi ufulu kuchita zionetserozo kuti aonetse kusakondwa kwawoko ndipo polakwikwapo pakonzedwe.

Nayo T/A Nkukula ya ku Lilongwe idati ngati magulu okhudzidwawa adakambirana pazolakwikazo n’kulepherana, zionetsero n’zosalakwika.

Related Articles

Back to top button