Zipani za moyo zioneke—CMD

 

Kodi zipani zinazi zili moyo? Nthawi yofukula yakwana m’zipani pamene bungwe loona mgwirizano wa zipani zosiyanasiyana la Centre for Multiparty Democracy (CMD) lalengeza zokumana ndi akuluakulu a zipani.

Bungweli laitana zipani 41 zomwe zidalembetsedwa koma zilibe aphungu m’Nyumba ya Malamulo.

CMD ikuchita izi kutsatira kudutsa kwa bilo yokamba za kayendetsedwe ka zipani imene mwa zina ikuti zipani zimene sizikuoneka zichotsedwe m’kaundula pakatha miyezi 12.

Tenthani: Tiwaimbira

Kalata yomwe CMD yatulutsa ikuti eni zipanizo atumize ku bungwelo maina a mtsogoleri wawo ndi mlembi—atumizenso nambala, madera amene akukhala.

Mkulu wa bungwelo, Kizito Tenthani adati zipanizo zikatumiza maina ndi manambalawo adzawaimbira kuti akumane nawo kuti awafotokozere zomwe zili m’biloyo.

Iye adati: “Ngati satiyankha mwina zisonyeza kuti kulibe munthu. Pakatha miyezi 12 ndiye kuti zisonyeza kuti chipanicho chazimirira—kusonyeza kuti osindikiza zipani atha kuchifufuta.”

Mwa zipani zomwe zaitanidwa ndi cha The Malawi Democratic (MDP) chomwe mwa ena amene adachiyambitsa ndi Kamlepo Kalua yemwe lero ali ku PP.

Chipani china ndi cha Malavi People’s Party (MPP) chomwe adayambitsa ndi Uladi Mussa amene akungoyendayenda. Adali ku UDF asadasinthe golo kupita ku DPP. Madzi atachitako katondo adalumphamo kugwera mu PP, lero wasinthanso golo kubwerera ku DPP.

Titamuimbira foni ngati alembere bungweli monga iye mtsogoleri, Mussa adayankha modabwa. “Malavi ndiye chiyani?” adafunsa. “Aaa! Nanga ine mesa ndidachokako, ndidali ku PP pano ndili ku DPP. Inuyo mungopitako mukaone atsogoleri amene apitawo osati muzindifunsa ine,” adatero.

Koma Tenthani ali ndi chikhulupiriro kuti zipanizi ziwalembera. “Ine ndi mkulu wa CMD, nditachoka lero sizikutanthauza kuti CMD yatha, atsogoleri otsalawo ndiwo angayankhepo ngati atafunidwa. Titsimikiza kuti m’zipanizo mudatsala ena amene atilembere,” adatero.

Mndandanda wa zipanizi ndi womwe udalembetsedwa m’dziko muno kuti ndi zipani zokhazikika.  Zina mwa zipani zoitanidwazo zidamveka pachisankho cha 1994 osamvekanso. Izi ndi monga cha Congress for the Second Republic cha Kanyama Chiume, Malawi Democratic Union cha Amunandife Mkumba, United Front for Multiparty Democracy, Malawi National Democratic Party ndi zina zotero.

Dziko lino lili ndi zipani zoposera 50.

 

Share This Post