Nkhani

Ziphuphu m’kalembera

Pamene kalembera wa unzika za dziko lino ali mkati, zadziwika kuti anthu ena apeza mpata wosolola m’matumba mwa Amalawi omwe akutenga nawo gawo lolembetsa mukalemberayu.

Amalawi ena akumafunsidwa kupereka K500 kapena kuposera apo kuti apeze mwai wa fomu yolembapo mbiri yawo. Izi zikumachitika makamaka pamalo akalemberayu pakakhala khwimbi la anthu omwe akumauzidwa kuti mafomu atha ndipo apereke kangachepe kuti ziwayendere.

Mwachitsanzo, Lachiwiri lapitali apolisi m’boma la Dowa adatsekera ofesala wa bungwe lomwe likuyendetsa kalemberayu la National Registration Bureau(NRB) yemwe amayang’anira ntchitoyu pa malo akalembera a Chuzu, kwa Traditional Authority(T/A) Nkukula m’bomalo pomuganizira kuti amalandira ziphuphu.

Ena mwa anthu omwe amalembetsa pamalopa amauzidwa kuti mafomuwa atha ndipo apitenso tsiku lotsatira ndi K500, ndipo mafomuwa akumatulukadi.

T/A Nkukula adavomereza kuti apolisi atsekeranso munthu wina yemwe adapita pa malo a Chuzu ndi kutenga mafomu atatu ponena kuti ena ndi a abale ake kunyumba koma amatsatsa mafomuwo pa mtengo wa K500.

“Komanso masiku apitawo chifukwa cha mitambo makina a kalemberayu adalibe moto choncho anthu ena adasonkha ma K200 n’kukagula maunitsi a magetsi omwe adatchajira makinawa kuti zinthu ziyende,” adatero Nkukula.

Komatu si ku Dowa kokha chifukwa nako ku Dedza ziphuphu zikuperekedwa kuti anthu ena apeze mwai olembetsa nawo mkalemberayu.

Malinga ndi mzimai wina wochokera pa malo a kalembera a  Katsekaminga yemwe adapempha kuti tisamutchule dzina lake, adapereka K500 kwa mfumu ina mderali kuti apeze mwai wa fomu yolembapo mbiri yake. Polankhulapo T/A Kamenyagwaza wa m’boma la Dedza adati ngakhale

kalemberayu wayenda bwino mmalo ena, vuto lalikulu lili pamalo a kalembera a Bembeke pomwe anthu akuvutika kuti apeze mafomu.

“Anthu ozungulira pa Bembeke akumauzidwa kuti mafomu atha ndipo akumakapempha pamalo ena a Liberito komwe mphekesera yandipeza yoti

akumawatchaja kangachepe,” adatero Kamenyagwaza.

Ndipo mneneri wa bungwe loyang’anira kalemberayu Norman Fulatira adavomereza zoti bungweli lalandira madandaulo a ziphuphu m’malo ena. “Tikupempha Amalawi akufuna kwabwino kuti azititsina khutu za mchitidwewu ndipo ife mogwirizana ndi apolisi tidzachita kafukufuku,” adatero Fulatira.

Iye adatsimikizanso za kutsekeredwa kwa ofesala wawo wa pamalo a kalembera a Chuzu.

Ntchito ya kalembera wa unzika idayamba mwezi wa May ndi cholinga chofuna kuti mwazina nzika za maiko ena zisamalandire nawo thandizo lopita kwa Amalawi monga m’zipatala zomwe zili m’malire a dziko lino ndi maiko ena.

Related Articles

Back to top button