Nkhani

Zitupa zaunzika zina zasowa

Listen to this article

Zitupa 93 893 za uzika m’boma la Kasungu zasowa. Tamvani itha kuvumbulutsa.

Izitu zadziwika pamene bungwe lolembera unzika la National Registration Bureau (NRB) layamba kupereka zitupazi kwa eni.

Mneneri wa wa bungwe la NRB Norman Fulatira watsimikiza izi ndipo wati: “Ili si vuto lalikulu mtima ukhale mmalo.”

Maboma amene adayambirira kulembetsa za unzika a Mchinji, Dowa, Kasungu, Salima, Nkhotakota ndi Ntchisi ayamba kulandira ziphaso zawo zomwe zaonetsa kuti nkhope zina zikusowa.

Anthu 93 893 amene amayembekezera kulandira zitupazi adadzidzimuka kuona kuti maina awo palibe pamene anzawo nkhope zawo zatuluka ndipo alandira zitupa.

Anthu amene dzina lawo lasowa m’bomalo ati chiyembekezo chawathawa ngati angalandire zitupa zawo.

Lufeyo Mwanza wa m’bomalo adauza Tamvani kuti chikhulupiriro pa NRB achotsa kuti zitupa zawo zidzapezeka.

“Inde akutilimbitsa mtima kuti zitupa zathu zibwera komabe chilimbikitso chimenechi nchosakwanira. Tikuganiza kuti zasowa ndipo mwayi wokhala ndi zitupazi watiphonya,” adatero Mwanza.

Iye adati pakhota nyani mchira nkuti anzawo amene adajambulitsira limodzi zitupa zawo zatuluka koma iwo zavuta.

Komabe Fulatira akuti mwa maina 1.7 miliyoni omwe adalembedwa moyambirira, mayina 1.5 miliyoni okha ndiwo adatumizidwa kuti akatulutse zitupa ndipo maina enawo amaunikidwa ngatidi ali a Malawi.

“Anthu [asathamange magazi] kuti zitupa zawo zasowa, chifukwa tikukonza ndipo alandira zonse zikatheka bwinobwino,” adatero Fulatira.

Iye adatinso zitupa 200 000 za m’ndime yoyamba ya kalemberayu ndizo sizidakonzedwe ndipo anthu omwe zitupa zawo zasowawo akhoza kukhala m’gululi.

“Pologalamuyi ndi ya a Malawi choncho timayenera kuunika maina bwinobwino kuti tisapezeke zoti tikupeleka ziphaso kwa alendo. Zonse zikatheka, aliyense yemwe ndi nzika ya dziko lino ndipo adalembetsa, adzalandira chiphaso,” adatero Fulatira.

Senior Chief Kaomba ya m’boma la Kasungu idati iyo siyikuonapo vuto pa nkhaniyi chifukwa zitupa zomwe zikusowa nzochepa poyerekeza ndi zomwe zapezeka.

“Aka nkoyamba boma kupanga kalembera ngati uyu ndiye pa mayina 1.5 miliyoni, kusowa maina okhawo si chodandaulitsa kwenikweni ndipo tikuyenera kumvetsetsa,” adatero Kaomba.

Iye adapempha anthu kuti adekhe chifukwa NRB ikulongosola.

Boma lidakhazikitsa ntchito ya kalembera wa unzika kuti lizitha kuzindikira anthu ake makamaka powathandiza pa ntchito zofunika ngati za umoyo, maphunziro komanso kuwapeza mosavuta akasowa kapena kutsakamira mmaiko a eni.

Kalembera yemwe ali mkati pano adayamba pa 24 May chaka chino ndipo akuyembekezeka kutha mu December.

Malinga ndi Fulatira, ntchitoyi idzakhala ikupitilira mpaka kalekale.

“Iyi idali ndime yokhazikitsira ndipo aliyense amayenera kulembetsa mmalo omwe tikuchita kukhazikitsa koma kuyambira January chaka chamawa, omwe sadalembetse, aziloledwa kukalembetsa mmaofesi athu a m’maboma kapena kotumizira makalata [post office] yomwe angayandikane nayo,” adatero Fulatira.

Iye adatinso amene ayambe kulembetsa chaka chamawa koyamba azidzalembetsa ulere pamene kwa omwe adasowetsa chitupa ndipo akufuna china, azidzapemphedwa kupereka kangachepe.

Kwa amene amakhala kutali ndi post office sadzavutikanso chifukwa NRB idzidzayendera m’madera kuthandiza Amalawi malinga ndi Fulatira.

Related Articles

Back to top button