Chichewa

Zovula pa Wenela ayi, tamva!

Listen to this article

 

Tsikulo pa Wenela padali ziii! Moti ojiya, osolola ndi osenza onse adali khumakhuma. Ndalamatu ndalama zalowa ku silent ndiye anthu sakuyenda.

Basi ya Lilongwe imatenga tsiku lonse kuti idzadze. Ambirinso amachita kunenera.  Nchifukwa chake ndidangoganiza zolowera malo aja timakonda pa Wenela. Ndidakapeza Abiti Patuma ndi Gervazzio akumvera nyimbo ya Lucius.

Poti sitima, imaphweka akamayendetsa wina….

Sindikudziwa kuti nyimboyo adayiika chifukwa chiyani!

Abiti Patuma adali bize pafoni yake.

artrt

“Koma abale, phungu uyunso ndiye amangokhalira pa Facebook. Taonani lero akuti iye sakufuna kukwezeredwa ndalama. Ndidakuuzani kale kuti uyu wokonda kuvina kanindoyu amangofuna kuti anthu azimumvera.

“Mwaiwala zija ankanena zolodza azungu osakaza la Mulanje phiri; mwamuiwala kuti ngwa nthabwala basi?” adatero Abiti Patuma.

“Zoona. Amati avula, ayende tauni ya Lilongwe onse aone kuti iye ndi munthu wamkulu, wotamba masana likuswa mtengo! Chomwe ndikudabwa nchakuti kodi bwanji phunguyu amachita zosiyana ndi aphungu ena?

“Akamabwera ku Nyumba ya Malamulo amakwera Bajaj, inde galimoto kaya ndi njinga ya matheyala atatu? Saona anzake akayenda pa galimoto zopuma ngati olemekezeka? Uyutu uyu kupanda kusamala naye adzalaula ndi pa Wenela pano!”

Adayankhira Gervazzio: “Ndikuona ngati nzeru zikumuchepera ameneyu, mwina zamuchulukira kwambiri?”

Abale anzanga, kunena zoona wamisala adaonadi nkhondo!

Posakhalitsa tindangoona  uyo watulukira atavala mwado wofiira wopanda lisani. Kumtundaku malayanso ofiira koma odula mikono. Tsinya lili gaa pankhope. Kenaka adayambitsa nyimbo, amvekere: Zivute, zitani ife Amalawi…!

Chigulu chidali chitasonkhana kuti chione munthu adalonjeza kuti avula uja, chidayankhira: Tili pambuyo pa maalubinoo!

Kenaka tidamva ali Left! Right! Left! Right…

Wayambika wa ndawala! Kuguba ulendo wa ku Nyumba ya Malamulo.

“Indetu ndinena ndi inu aphungu anzanga. Dziko lafika pena. Lamulo ligwire ntchito. Diso kwa diso, mphuno kwa mphuno! Akakumenya mbali inayi, nawenso menya! Tatopa ndi ulemu…Ndiponso a AI, fokofu, akagwere ku Gahena! Asaa! Ati tisaphe wopha alubino, zamkutu!”

Musandifunse kuti a AI ndani, poti nane sindikuwadziwa ndipo olo nditawadziwa sindingakuuzeni. Nanga ndichite kukuuzani kuti ndi aja, aja adabwera aja, kodi mumati andani paja?

Kenaka munthu adavala mwado uja adayamba kulira ngati mwana! Palibe adaseka. Ndidayang’ana Abiti Patuma…nawonso adagwetsa tsozi!

Gwira bango, upita ndi madzi mwaiwe! n

Related Articles

One Comment

  1. Ine ndinamva anthu ena anali pambali pa nseuwo posiliza nyimboyo: “zivute, zitani, ife aMalawi”, amayankha “…tili pambuyo pa Kamuzu.” Asaa!
    Kodi anthu amenewa anali a MCP olo ongofuna kusokoneza dziko? Zigawenga?

Back to top button