Nkhani

‘Ngakhale panali zovuta, chisankho chayenda’

Listen to this article

Bungwe lophunzitsa Amalawi zosiyanasiyana kuphatikizapo za demokalase la National Initiative for Civic Education (Nice) lati ngakhale chisankho cha chaka chino chinakumana ndi mikwingwirima, chidayenda bwino.

Povumbulutsa zimene bungwelo lidapeza pa momwe chisankhocho chidayendera ku hotela ya Victoria mumzinda wa Blantyre Lachinayi, mkulu wa bungweli Ollen Mwalubunju adati Amalawi ayenera kudekha podikira chisankho chimene chidachitika Lachiwiri.

Ollen Mwalubunju
Ollen Mwalubunju

Pofika Lachinayi, zotsatira za chisankhocho zidali zisadalengezedwe ndipo madera ena adali asanamalize kuvota.

“Chisankhochi chakumana ndi mikwingwirima monga kusowa kwa zipangizo zina, zimene zidachititsa zipolowe m’madera ena. Koma zonse zili apo, chisankhocho chidayenda bwino,” adatero Mwalubunju.

Malinga ndi Mwalubunju, Amalawi ayenera kudekha poyembekeza zotsatira za chisankhocho chifukwa kuchita phuma kukhoza kudzetsa mavuto.

“Tiyamike a MEC chifukwa pamene pamakhota, iwo samachedwa kupakonza. Umu ndiye ziyenera kukhalira,” adatero Mwalubunju.

Chisankho cha Lachiwiricho chidali cha chisanu kuchitika m’dziko muno kuchokera pamene kudadza ndale za zipani zambiri. Pamene timalemba, nkuti wopambana asadadziwike.

 

 

Related Articles

Check Also
Close
Back to top button