Nkhani

‘Sibwino kulekeza panjira kumwa ma ARV’

Listen to this article

Mmodzi mwa anthu amene adapezeka ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ndipo akukangalika kuphunzitsa ena za matendawa Hannah Mandanda wati ntchito yolimbikitsa anthu amene akulandira ma ARV kuti asasiye kumwa mankhwalawa ndiyaikulu.

Polankhula pamaphunziro amene bungwe lothandiza  anthu amene adawapeza ndi kachilombo la Dream ku Balaka, Mandanda adati kusiya kumwa mankhwala kwadzetsa imfa zomwe sizikadakhalapo.

“Anthu ena amalandira mankhwala koma osamamwa. Uku n’kulakwa. Masiku apitawa, tidali ku maliro a mayi wina amene ngakhale ankalandira mankhwala mwezi ndi mwezi, amangowabisa kuchipinda ndipo tidawapeza atatisiya,” adatero Mandanda.

Mkulu woyang’anira ntchito za Dream ku Blantyre, Jane Gondwe, adati vuto la odwala kuleka kumwa mankhwala likukulira kulira.

“Ena amasiya chifukwa achipembedzo awauza kuti Mulungu wawachiritsa pomwe ena amanamizidwa ndi asing’anga. Enanso amasiya chifukwa chitetezo cha m’thupi mwawo chakwera koma ayi sichoncho. Mankhwalawa ndi akumwa moyo wonse,” adatero Gondwe.

Iye adati ena amasiya kumwa ndipo akaona kuti matenda ayambanso kuvuta amayambiranso kumwa mankhwala.

“Koma palibe chimene angaphule chifukwa kachilombo kamakhala kuti kakhwima ndi kupeza njira zina kuti mankhwalawo asagwire ntchito,” adatero Gondwe.

Iye adati n’chifukwa chake bungwe lawo limaphunzitsa anthu 65 woti azikaphunzitsa ena momwe angadzisamalire atawapeza ndi kachilombo ka HIV.

Related Articles

Back to top button