Nkhani

‘Wogona’ ndi mwana wake pofuna mfumba agwidwa

Listen to this article

Ndani adanena kuti chizimba cha mfumba ndi kugona ndi mwana wako? Izi zachitika ku Dedza komwe apolisi anjata bambo wa zaka 49 pomuganizira kuti adagona ndi mwana wake, wa zaka 17, kuti achulutse zokolola.

Tikunena pano akuti mkuluyu wapha kale ngolo ziwiri za chimanga pomwe zaka zapitazi ankakolola osakwana ndi ngolo imodzi yomwe. Iye wati wangokolola theka chabe la mundawo.

Njondayi, Levison Dickson, ya m’mudzi mwa Chimalira kwa T/A Kachere m’bomalo, akuti ili ndi ana asanu ndi mmodzi (6), amuna awiri akazi anayi. Idagona nayeyu akuti pano ali ndi mthunzi wa miyezi isanu.

Mneneri wapolisi ya Dedza, Edward Kabango, wati Dickson adauza apolisi kuti adapita ku Mozambique kukasaka mfumba yoti ulimi wake wa mtedza, chimanga, soya ndi nyemba uzimupatsa zokolola zamnanu.

“Adati kupatula kutsira fetereza ndi kusamalira zokolola zake pamayenera mfumba igwire ntchito. Adauza apolisi kuti anthu ena akuchita zimenezi ndipo zikuwayendera,” adatero Kabango.

Mneneriyu adati mkuluyu atafika m’dzikolo adakumana ndi ng’anga yomwe idamutemera mterawo koma chizimba chake kudali kukapumira pamwana wake mpaka mwanayo atakhala ndi pathupi.

Ntchito yokwaniritsa chizimbacho akuti idayambika mu January chaka chino. Akuti mlimiyu adamasuka chifukwa mkazi wake n’kuti ali kwa apongozi ake komwe amachereza matenda.

Kabango wati mkazi wa mkuluyu atabwera adadabwa ndi momwe msungwanayu amaonekera chifukwa amaonetsa zizindikiro zoti ali ndi pathupi.

“Mayiwo adamupanikiza ndipo adaulula kuti bambo ake ndiwo mwini wa pathupipo. Iye adawauza kuti bambowo adamuuza kuti agone nawo kuti akolole zochuluka.

“Mayiwo atadzatifotokozera izi pa 25 May tidanjata mkuluyu. Iye adavomereza kuti adagonadi ndi mwanayo kuti kumunda akolole dzinthu dzochuluka,” adatsindika Kabango.

Woganiziridwayu adakawonekera kubwalo la milandu Lachinayi lapitali komwe iye adavomera mlanduwo.

Chilango cha mlanduwu ndi kukakhala kundende zaka zisanu. “Zimatengera momwe mlandu wakhalira. Malamulo amati ngati msungwanayo adali wosaposa zaka 16, woganiziridwayo akaseweze moyo wake wonse, zakazi zingasinthe ndi momwe woweruza mlandu angagamulire,” adatero Kabango.

Related Articles

Back to top button
Translate »