Chichewa

Anatchereza

Listen to this article

Amandimenya

Anatchereza,

Ndine mtsikana wa zaka 19 ndipo ndili ndi bwenzi la zaka 21 yemwe ndili naye mwana mmodzi. Dandaulo langa ndi loti akandipeza ndikucheza ndi anyamata amandimenya ngakhale kuti sitinakwatirane. Koma iyeyo amachezanso ndi atsikana ena koma ine sindiyankhulapo kanthu. Nthawi ina adandimenya mpaka kukomoka. Nditani agogo anga?

LWT,

Chilobwe, Blantyre

 

LWT,

Ndamva vuto lako, mwana wanga. Kuchitirana nkhanza m’banja kaya pachibwenzi si chinthu chololedwa ngakhale pang’ono ndipo aliyense wochitira mnzake nkhanza zamtundu uliwonse akulakwira malamulo ndipo atasumiridwa ayenera kulangidwa ameneyo. Zimatheka bwanji kuti anthu okondana azichitirananso nkhanza pomenyana? Wachita bwino kubweretsa vuto lako poyera chifukwa alipo ena amene akumachitiridwa nkhanza ndi okondeka awo koma zimangothera m’mimba, ati kumenyana ndi mankhwala a banja. Si zoona zimenezi. Tsono iwe utamenyedwa ndi bwenzi lakolo mpaka kukomoka basi udangokhala duu! Nawenso ndiye kuti ndi wopepera! Adzakuphatu ameneyo ukapanda kusamala naye. Zikadzachitikanso uyenera kukamuneneza kupolisi kapena kumabungwe amene amayang’anira za maufulu a anthu kuti adzakuthandize chifukwa akukuphwanyira ufulu wako ameneyo. Nditengerepo mwayi wolangiza achinyamata kuti kukhala ndi ana musadalowe m’banja zotsatira zake zimakhala ngati zimenezi. Chibwana basi! Zichepe chonde.

 

Ndikumukondabe

Zikomo Anatchereza,

Ndine bambo wa zaka 30 ndipo ndili ndi ana awiri. Vuto lomwe ndili nalo ndi loti mkazi ndinabereka naye ana anandithawa miyezi 11 yapitayo ati ndimamuvutitsa. Pakalipano ndapeza mkazi wa zaka 20 ndipo akunetsa kuti amandikonda. Ndinamuuza chilungamo chonse chokhudzana ndi ana ndipo adamvetsa. Ndithandizeni maganizo poti wakaleyo ndimamukondabe limodzi ndi ana anga. Koma wapanopayunso ali ndi pathupi panga. Ndithandizeni chonde.

ZTB

 

ZTB,

Nkhani yanu ndi yovuta ndipo sindidziwa kuti ndikuthandizani bwanji. Choyamba mwanena kuti mkazi wanu woyamba amene muli naye ana awiri adakuthawani chifukwa ati ndinu wovuta. Kuvuta kwake kotani? Inu mukuti mumamukondabe ndi ana, koma pano mulinso pachibwenzi ndi mayi wa zaka 20, yemwe pano ndo woyembekezera. Mafunso nawa: Ngati mkazi adakuthawaniyo mumamukondadi, mudachitaponji kuti mubwererane? Ngati mumamukondadi, chidachitika n’chiyani kuti mugwenso m’chikondi ndi mtsikana wa zaka 20 mpakana kumupatsa pathupi musanamukwatire? Chimene ndikuona apa ndi chinyengo kumbali yanu ndipo ndinu wovutadi abambo inu. Ndinu wachimasomaso n’theradi! Poti munthu sudziloza chala, mwina mkazi wanu woyambayo adaona kuti ndinu wovuta ndi nkhani yokonda akazi koma muli pabanja. Tsono ngakhale mutabwererana ndi mkazi adathawayo, nanga mwana wa eni mwamutupitsa mchomboyo mumutani? Zofunatu izo! Mukuvutitsa ana osalakwa, za zii!

 

Ndikufuna bambo anga

Anatchereza,

Ndine Efrida Lungu kwa Kayembe, T/A Wimbe ku Kasungu. Ndimangomva kuti bamboo anga ndi a Lungu, Achitumbuka ndipo akuti alipo. Ine ndimafunitsitsa nditawaona. Akuti ankaphunzitsa pa Chamama School ndi pa Chimbowe. Akuti adandisiya ndili ndi zaka ziwiri koma pano ndili ndi zaka 19 ndipo ndili Form 4. Amene angawadziwe chonde tilumikizane pa 0999 810 665/0885 831 843/0997 249 347 . Ambuye akudalitseni.

 

Ofuna banja

 

Ndine mayi wa zaka 26 ndikufuna mwamuna wa zaka 28. Ndili ndi mwana mmodzi. Mwamunayo akhale Mkatolika. Wondifuna aimbe pa 0884 484 963.

 

Ndili ndi zaka 24 ndipo ndikufuna banja, Ndili ndi mwana mmodzi ndipo kwathu ndi ku Kasungu. Nambala yanga ndi 0884 144 638 . n

Related Articles

Back to top button